Alira Chokweza pa Msika Kamba Kopheledwa Njoka

Mkulu wina yemwe amachita geni ya wokala pa msika wa Makhetha ku Machinjiri munzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre akuti masiku apitawa anadabwitsa anthu pamene analira chokweza atazindikira kuti anthu ena pamsikawo apha njoka yomwe imadutsa kuseli kwa mawokala ena.

Malinga ndi kunena kwa bambo Mikeyasi omwe amachita geni ya nsomba za manyalira pa msikawo, nkhaniyi akuti inachitika masiku apitawa pamene anthu mumsikawo amadabwa ndi m’mene geni ya mkuluyo imapitira patsogolo kamba koti anayamba ndi kakhobili kochepa zaka zapitazi.

‘Anthu akhala akuyamba geni pamsika umenewu zosiyana siyana koma ambiri amathawa kukachitira kwina kamba koti pali zikhulupiliro zoti anthu ena amachita geni zawo pogwiritsa ntchito matsenga. Tsopano chomwe chinadabwitsa anthu patsikuli nkuti mkuluyo anauza anzake kuti satsegula sitolo yake kamba koti amafuna kukagwira ntchito za kumunda monga mukudziwa kuti anthu ali mkati mobzala chimanga ndi mbeu zina,’ iwo anafotokozera Maravi Express motere.

Koma mkuluyo akuti atanyamuka pa njinga ya kabanza ulendo wa kumunda kwake, anthu pamsikawo anawona njoka ikudutsa kuseli kwa mawokala ena ndipo mosakhalitsa anayamba kuyigenda mpakana kuipha.

Atatero anthuwo anaganiza zoyibutsa moto ndipo atangotero akuti mkuluyo anatulukira pa msikawo nkuthamangira muwokala yakeyo koma akukhetsa nsonzi ngati kuti waonekeledwa zovuta.

Kenaka mkuluyo akuti anatuluka muokalayo madzulo mdima utayamba ulendo kunyumba kwake koma nkhope itagwa pansi kwinaku akupukusa mutu.

Malinga ndi a Mikeyasi, anthu ochita malonda pamsikawo akuti akuganiza kuti mkuluyo amachita bizinezi yake kudzera m’matsenga komanso kuti ankagwiritsa ntchito njokayo kuti izinka ikawa ndalama za anthu ena pamsikawo.

Padakali pano mkuluyo akuti pawokala yakeyo sipakuzadzanso anthu ngati kale kamba ka mbiri ya nkhaniyi yomwe yafala kwambiri pamsikawo.