Ophunzira akale a Kamuzu Academy apeleka thandizo la zotetezera ku Coronavirus ku zipatala zitatu zazikulu
Wolemba Duncan Mlanjira Ophunzira akale a Kamuzu Academy, ataunikira kuti omwe akuthandiza kwambiri kuti muliri wa Coronavirus usafalikire kwambiri ndi ogwira ntchito mu zipatala, anasonkhanitsa ndalama ndikugula zipangizo zoti akatswiri a zaumoyowa nawonso atetezedwe ku matendawa. Akatswiri a zaumoyo alinso pa chipsyezedwo choti nawonso akhoza kudwala chifukwa chopatsikiridwa kuchokera kwa odwala omwe angapezeke kuti akuwathandiza. Zinthu zomwe zidagulidwa ndikuperekedwa ku zipatala zazikulu m’dziko muno — ku Queen Elizabeth, ku Kamuzu Central and ku Mzuzu Centre — zinali magawuni 400;…