Mkulu wina kwa Bvumbwe mboma la Thyolo akuti akuyenda zolizoli ngati nkhuku ya Chitopa kamba ka manyazi atamupezelera akuchita za dama ndi msungwana woyendayenda kuseli kwa malo ena omwera chakumwa chaukali.
Bambo Misheck omwe anawona izi zikuchitika maso ndi maso masiku apitawa anafotokozera Maravi Express kuti mkuluyo wakhala akuchita mchitidwewu mozembera mkazi wake yemwe anamubelekera ana atatu.
Ndiye paja akulu amati ukatambatamba udziyamba kaye wayang’ana kunyanja kamba koti kunja kungakuchere, iye anawona ngati kutulo pamene anthu ena omwe ankamwa nawo mowa pa tsikulo anatsina khutu mkazi wake kudzera pa lamya ya m’manja kuti watengana ndi msungwana wina woyendayenda kupita kunyumba kwake yomwe ili pafupi ndi balayo.
Mkazi wakeyo atangomva izi analiyatsa liwiro kuthamangira kunyumba kwa msungwana woyendayendayo ndipo atafika anangotsegula chitseko nkupeza awiriwo ali pa mphasa kuchipinda akuchita za dama zawozo.
Kenaka chindeu akuti chinabuka pakati pa mwini banjayo ndi msungwanayo ndipo mosakhalitsa khwimbi la anthu linasonkhana pa nyumbayo kwinaku nawo amayi ena akuthandiza mwini banjayo kulanga chimbalangondocho chomwe akuti anachivula zovala zonse mpakana chinochino kwinaku magazi ali chuchuchu mkamwa ndi mphuno momwe.
Nkhope ya msungwana woyendayendayo akuti inatupanso ngati wagundidwa ndi sitima ndipo anzake omwe anthu akuwaganizila kuti amachitanso khalidwe lonyasali ndiwo anayesetsa kumupulumutsa pomuveka chitenje nkumuthawitsa pa malowo.
M’mene izi zimachitika nkuti mkulu wachimasomasoyo atathawa ndi kabudula wa mkati yekha ulendo kunyumba ndipo atafika anangotenga ka chikwamaka tizovala take ulendo kwa mzake yemwe amakhala ku Machinjiri mumzinda wa Blantye.
Padakali pano maiyo wanenetsa kuti za banja palibenso ndi mkuluyo yemwe m’mene timatsindikiza nkhaniyi nkuti zamveka kuti wabweleranso kwa Bvumbwe komwe akupanga lendi pa mudzi wina kumeneko.