Ayaluka Atapezeleredwa Akuchita za Dama ndi Mwana Omupeza

Zina ukamva akulu sadalakwitse ponena kuti kamba anga mwala. Mkulu wina yemwe akuti wakhala akunka alalikira malo osiyana-siyana mtauni ya Limbe pomadzitcha kuti ndi mneneli akuti masiku apitawa wayaluka pamene anamupezelera akuchita za dama ndi mwana wake omupeza ku bafa. Izitu zachitika ku Nthandizi mtaunishipi ya Bangwe.

Malinga ndi kunena kwa bambo omwe anangozitchula kuti ndi a Macheso omwe amakhala pafupi ndi nyumbayo, iye wakhala akukayikitsa anthu za mayendedwe ake akamachoka pakhomo kupita mtauni ya Limbe kamba koti masiku ambiri amauza mwana omupezayo kuti amunyamulire chikwama mpakana ku sitenji kenaka azikakonzeka zopita ku sukulu.Akamabwera ku sitejiko akuti iyayi amakhala ndi kangachepe komwe amatha kugula chipisi ndi saladi kusukulu modabwitsa anzake.

Mayi wa panyumbapo akuti wakhala akuuzidwa za khalidwe la bamboyo kuti zimakhala ngati amayenda mwamseli ndi mwanayo koma iye samazitengera chifukwa nthawi zambiri amalawilira ku misika ya Nkando komanso Bvumbwe komwe amakapikula ndiwo zakudimba kumanka agulitsa mtaunishipi ya Bangweyo ngati imodzi mwa njira zothandizira kuchepetsa zina mwa zosowa za pa banjapo.

Kenaka akuti patsikuli, mkuluyo yemwe wangobelekera mkazi wakeyo mwana wakhanda miyezi ingapo yapitayi anafika pakhomopo cha ku madzulo mdima utangoyamba ndipo anauza mwana omupezayo kuti amutenthetsere madzi osamba ndipo mwanayo anachita motero.

Koma mkuluyo atangolowa mbafa anayitana msungwanayo kuti amupititsire siponji ndi sopo zomwe anayiwala koma chonsecho ali ndi cholinga chokafuna kupitiliza khalidwe lake lonyasa lomagona ndi msungwanayo mkazi wake akachoka pakhomopo.

Mwanayo akuti atangolowa m’bafamo mkuluyo anayamba kuchita naye zadamazo osadziwa kuti mkazi wake wafika pakhomopo ndipo atatsegula mnyumba anawona kuti mulibe munthu. Kenaka chosadziwa atangoona chikwama cha mamuna wakeyo anapita kubafa kuti akawone ngati mwina amakayimilira.

Maiyo akuti anangoti gwejuuu! chitseko anawona ngati kutulo pamene anapeza malodzawo ali mkati ndipo mosataya nthawi anayamba kukuwa kwinaku akulira chokweza ngati waferedwa. Mkuluyo apa anadziwa kuti zake zada ndipo akuti anangoti buluku lake tolu nkuyamba kuthawa panyumbapo.

Nayenso msungwanayo akuti anangoti kakasi kusowa chochita mbafamo ndipo mayi wina woyandikana naye nyumba ndi yemwe anachita machawi populumutsa mwanayo kwa anamalira olusa omwe amafuna kulanga onse ati kamba koyalutsa mudziwo.

Padakali pano, malipoti akuti mkaziyo wasesa katundu yense mnyumbamo ndipo wakamusungitsa kwa mkulu wake ku Masala mtaunishipi yomweyo ya Bangwe.