
Mayi Nellie Mkhumba ndi Tcheya ndi owulutsa nkhani, bambo Ben Mitochi
* Boma likalephera kupeleka ndalama yo pofika kumapeto a mwezi wa August 2025 azatsatira njira zina monga kupita ku khothi
* Kapenanso kuchita zionetselo za bata ku ma ofesi Tresuary ku Capital Hill ku Lilongwe kuyambira lachiwiri pa September 2 osachoka mpaka onse atalipidwa
Wolemba Duncan Mlanjira
Omwe ankagwira ntchito m’boma (civil servants) amene anapuma ntchito (Penshoniya) kuyambira 2022 mpaka 2025, akuvutika kwambiri chifukwa sanalandilebe ndalama zawo za pensoni.

Advertisement
Ndipo awuza Boma la Malawi kuti “liyenera kulipira ndalamazi ndi chiongola dzanja (interest) nsanga, komanso likufunsidwa kuti kulipirako kuchitike ndikutha pofika kumapeto a mwezi wa August 2025”.
“Kulephera apo nde kuti ife titsatira njira zina monga kupita ku khothi kapenanso kuchita zionetselo za bata ku ma ofesi a Tresuary ku Capital Hill kuyambira lachiwiri pa 2 September 2025 osachoka mpaka onse atalipidwa.”
Izi ndi zomwe anakamba bungwe la ma Pensoniya la dzulo lachinayi mu Mzinda wa Blantyre kuchokera pa chikalata chomwe anawelenga pa msonkhano wa atolankhani.
Bungweli linakhazikitsidwa ndi kubvomerezedwa ndi Boma kuti azifikira anzawo amene m’ngosowa kuthandizidwa mtsogoleri wawo ngati Tcheya ndi mayi Nellie Mkhumba motsatizidwa ndi a secretary mayi Catherine Bandawo ndi owulutsa nkhani, bambo Ben Mitochi.

Mu chikalata chawo, komanso poitambasulira, bungweli lafika poyenera kunena kuti “Boma la Malawi likusungabe ndalama za ma Peshoniya amene anapuma ntchito mboma kuyambira 2022 mpaka 2025.”
“M’chitidwe umenewu waika moyo wa anthu opuma ntchitowa pa chiopsyezo ndi pa umphawi, womwe mwa zina ndikuphatikizapo:
1. Kulephera kupeza thandizo la makwala ku zipatala mthupi mukadwala, monga zili
zodziwikatu kuti matupi a anthu akulufe amakhala pa chiopysezo cha matenda pafupi pafupi;
2. Kulephera kupeza chakudya chathu ngakhalenso kudyetsa mabanja athu maka panopa pamene m’dziko muno muli bvuto lakusowa kwa chakudya m’madera ambiri kamba kabvuta la zanyengo ndi kukwera kwa zinthu;
3. Ana athu akusiya sukulu kamba kosowa ma fizi, Mabanja ndi abale athu amaganiza kuti tinalandila kale ndalamazo koma timangobisa kuti tizidya ndi kugwiritsa ntchito tokha; ndi
4. Kutsika kwa ndalama ya Kwacha ndalama zathuzo zili m’manja mwa Boma zapangitsa kuti zolandira zathu zikhale zochepa ndi zosathandiza chifukwa chakuchepa mphamvu kwa ndalama yolandilidwayo.

Ena mwa mamembala a bungwe la ma penshoniya
“Kuyesetsa mosatopa kwa ma Directors a Association yathu kulankhulana ndi mabwana a ku Treasury kuti alipire ma peshoniya onse amene ali oyenera kulandila ndalama zao monga mwa zolembedwa mmalamulo a za peshoni; zakhala zikuchitika koma osapindula kathu konse.
“Ife a bungwe tikuona kuti chinthu ichi mchofunika changu koma tikudabwa ndikukhumudwa kuona kuti Boma likungomatinamiza ngati ndife ana pomanena kuti panabwelekedwa K100 billion koma olandila ndalamazo kukhala anthu ochepa okha.
“Mapeshoniya atopano ndi zolonjeza zosachika, ndife okwiya kuona kuti ndalama zoyenera kuperekedwa kwa anthu opuma ntchitowa zalowera njira zina za ntchito za Boma,” iwo anatetero.

Advertisement
Poonjezera, aMitochi anayamikira kuti Boma likuwalolera kukambirana nawo ngakhale zakhala zosapindulitsa kwenikweni ndi chifukwa chake atazatsatire njira zinano ngati madandaulo awo sayankhidwa bwino pa nthawi yomwe aperekayi.
“Tikupemphanso Boma kuti atsogoleri athu apatsidwe mpata kuonana ndi a State President kukawatulira madando athu ndipo tikunenetsa zakufunikira koti Boma lilipire ndalama zowonjezera (interesta) kaamba kotsika mphamvu kwa ndalama ya kwacha.”
Bambo Mitochi anenanso kuti bungweli ndi mamembala akupempha Boma kuti “lisithe zoti Peshoniya akamwalira, anthu otsalawo adzalandire ndalama za miyezi 60, kuti lamulo lisithike kukhala theka lokha, mwini wakeyo alandiriretu theka linalo kuti athandizike ali moyo”.
Podziwitsa anthu onse za kukhazikitsidwa ndi kubvomerezedwa ndi Boma kwa bungweli aMitochi anati kufunikira kuti ena monga mabungwe ofunira zabwino awathandize ndi ndalama zogulira zipangizo za office ngakhale mathandizo ena otha kufikira ma Pensoniya anzawo amene akusowekera kuthandizidwa.
Ndiponso apempha mapeshoniya omwe sali ma membala potengera kuti ena sakudziwa kuti awafikire ndi kudzalembetsa umembala mu mkaundula mwawo.



Advertisement