Momwe chuma cha Malawi chilili pakali pano, boma lilibe ndalama zothandizira ndondomeko zongogawira anthu chabe
* Kodi adawona kuti kupereka MK500,000 kwa mwana aliyense wakhanda ndi njira yolondola? * Kodi iwo adaganiziradi mozama, potengera zenizeni ndi mavuto omwe dziko lathu likukumana nawo pa nkhani ya chuma? aChifipa Mhango, omwe ndi katswiri wamkulu wa zachuma omwe amagwira ntchito zounikira momwe maiko amayendetsera nkhani zachuma ayankhulapo za ndondomeko yomwe chipani cha Malawi Congress Party (MCP) yaika mu manifesto yake. Iwo ati: aMalawi anzanga, pa Lolemba, pa 21 July 2025 ndinali ndi mzimu wotaya mtima kwambiri nditatha…








