
Wolemba Duncan Mlanjira
Ophunzira akale a Kamuzu Academy, ataunikira kuti omwe akuthandiza kwambiri kuti muliri wa Coronavirus usafalikire kwambiri ndi ogwira ntchito mu zipatala, anasonkhanitsa ndalama ndikugula zipangizo zoti akatswiri a zaumoyowa nawonso atetezedwe ku matendawa.
Akatswiri a zaumoyo alinso pa chipsyezedwo choti nawonso akhoza kudwala chifukwa chopatsikiridwa kuchokera kwa odwala omwe angapezeke kuti akuwathandiza.

Mayi Lizzie Chikoti kupereka thandizo ku Queens
Zinthu zomwe zidagulidwa ndikuperekedwa ku zipatala zazikulu m’dziko muno — ku Queen Elizabeth, ku Kamuzu Central and ku Mzuzu Centre — zinali magawuni 400; ma epuloni 400; mamasiki a ku nkhope 1000; mamasiki a mu theatre 5,000; magolovesi 50,000 ndi mabotolo a hand sanitizer, 108.
Katunduyu anagawidwa m’zipatalazi mofanana. Kunali kobvuta kuti ophunzira akalewa angagule zonse zimene zikufunika potengera kuchepa kwa ndalama zimene zinapezeka.

“Choncho tagula katundu amene tawona kuti ndiwofunika kwambiri,” iwo anatero mofanana popeleka zidazi ku zipatala zonse zitatu Loweluka, June 6.
“Pofuna kudziwa kumene thandizoli lingapindule kwambiri tinakhazikitsa komiti yakuti ifufuze nkhaniyi ndipo kudzera mu kafukufuku ameneyu, kunapezeka kuti zipatala zazikulu (central hospitals) ndi zimene zikukhudzidwa kwambiri kuposa zina m’zigawo zonse.”

Ku Mzuzu
Anthuwa, omwe akugwira ntchito zotukula dziko lino mu njira zosiyana siyana — ena ngati madotolo, ma lawyer, ma judge, ma engineer, ma accountant ndi zina zambiri — adati amachitenga ngati chinthu cha mtengo wapatali kuti adapindula koposa pa kukhala ndi mwayi ophunzira ku sukulu yapamwambayi.
“Izi ndi molingana ndi masomphenya a Tate ndi Mkhazikitsi wa sukuluyi, president woyamba, malemu Dr Hastings Kamuzu Banda.

Kamuzu Academy
“Tili otsimikizika ndi mtima onse kuti ngati anthu amene tinalandila dalitsoli tiri ndi udindo wawukulu wowonetsa chiyamiko chathu pakubwezera ubwinowu ndi kupindulira anthu onse a m’dziko la Malawi m’njira zosiyanasiyana.
“Ngakhale kuti timakwaniritsa chifunirochi kupyolera m’mawudindo amene tili nawo a tsiku ndi tsiku, tikhulupilira kuti pali zina zimene zimatigwera zimene zimasowa kuti ali yense atengeko gawo pogwirana

Coronavirus alert
Iwo anatinso chiphyinjo cha COVID-19 chagwera dziko lino lomwe lili lomodzo laosauka kwambiri pa dziko lapansi.
“Pa chifukwa ichi, dziko lathu lilibe zipatala ndi zipangizo zoyenera ndi zokwanira kuti tingathe kulimbana ndi kuthana ndi mliriwu.
“Ndizodziwikiratu kuti wonse wogwira ntchito za chipatala ali pa chiwopsyezo chachikulu kwambiri pamene iwo ali nkukhudzidwa ndi ntchito yopima ndi ndikuthandiza anthu odwala ku matenda owopsyawa.

Coronavirus alert
“Chifukwa cha kuchepa kwa madotolo mdziku la Malawi, anthu zikwi makumi atatu (30,000) amadalira dotolo m’modzi kuti awathandize pa nkhani za umoyo ndi machiritso.
“Pa chifukwa ichi, ndikofunika kwambiri kuti tiwonetsetse kuti madotolowa komanso onse ogwira ntchito za chipatala akhale patsogolo kukhala ndi zonse zowatetezera ku matendawa pamene alinkugwira ntchito yofunikayi.
“Ntchito yopeza zipangizo zotetezera anzathu achipatalawa ndiyayikulu kwambiri; Boma palokha silingakwanitse. Ndikofunika kuti anthu ndi mabungwe osiyanasiyana athandizepo pantchito yopeza ndalama zogulira zipangizozi.

Coronavirus alert
“Ichi ndi chifukwa chake bungwe lathu lakhudzidwa kuti tithandizepo. Ngati bungwe laling’ono, tayesetsa kuthandiza boma pa kudziwitsa anthu za kuwopsya kwa matendawa.”
Kuti izi zitheke, gululi linapanga dongosolo lomema onse anaphunzira pa Kamuzu Academy kuti asonkhe kangachepe kuti papezeke ndalama zokwanira K20 million zogulira katunduyu.
“Choncho ngakhale kuti thandizo limene takonzali liri nkuperekedwa m’dzina la ophunzira akale a Kamuzu Academy, ndibwinonso kuti tinene kuti panali wena ambiri amene anatithandizako kupeza ndalama zimenezi.

Coronavirus alert
“Pa ichi tiri othokoza kwambiri ndi mtima onse kwa iwo amene atithandiza m’njira zosiyana siyana makamaka anthu ndi mabungwe a m’mayiko akunja ndi a mwathu mom’muno ngakhale kuti iwo simamamembala a gulu lathuli.
“Amene atithandizawo achita zimenezi mowolowa m’manja, osati poyang’ana ife ayi, koma pokhudzidwa ndikumvera chisoni mtundu wa Amalawi. Ndalama zimene tasonkha eni akefe kuphatikiza ndi zimene ena atithandiza nazo, zonse pamodzi zakwana K20.27 million.

Malemu Elsie Sazuze
“Tifuna tithokoze onse ogwira tchito za chipatala chifukwa cha kudzipereka kwawo polimbana ndi mliriwu. Mwapadera tifuna tipeleke ulemu pokumbukila onse amene atisiya pa dziko lonse la pansi ali mkati mogwira ntchito yothandiza onse wodwala ndi matenda owopsyawa.
“Amodzi mwa amene atisiya ndi a Malawi amene amagwira ntchito ku mayiko ena; iwo ndi mayi Elsie Sazuze, Dr Austin Gunda ndi bambo Grant Maganga.

Ulemu kwa a katswiri a zaumoyo
“Polemekeza ndi kuyamikila ntchito ya mayi Sazuze, anthu a chifundo a mdziko la Scotland athandizapo ndi ndalama zokwana £5,000 (zomwe zili zokwana K5 miliyoni).
“Iyi inali ngati ‘mphatso ku mtundu wa aMalawi’ popeleka ulemu kuti mayi Sazuze anamwalira pamene amagwira ntchito ya unamwino kuchipatala china ku UK ndipo anamwalira akuthandiza odwala matendawa.
“Ndipo anthu a ku Scotland akuyamika kuti mayi Sazuze anali munthu wa chikondi kwambiri pa ntchito yawo ya unamwino.

Coronavirus Alert
“Kupyolera mu imfazi, ife tinafulumizidwa kuti tichitepo kanthu pa kusonkhetsa ndalama zoti tigulire zipangizo zofunika kuti titeteze anzathu a chipatala. Mizimu ya onse otisiyawa iwuse mu mtendere.”
Iwo adatsikimizira kuti zomwe zaperekadwazi ndi gawo lochepa kwambiri chifukwa aliyense ali ndi udindo ochepetse bvutoli pakuyesetsa kutsatila malangizo onse amene a chipatala akutiuza zammene tingapewere kachirombo ka COVID-19.
“Ife tikakhulupilika pa kutsatira ndondomekozi ndiye kuti titetezanso anzathu a chipatala amene ali kale pa chiopysezo ndipo akuyesetsa kupulumutsa miyoyo.”