Adziyipitsira Pambuyo Pomwa Mowa Wachilendo

Mkulu wina ku Bangwe akuti akuyenda werawera pambuyo podziwonongera kamba koti anamwa kwambiri mowa wina wachilendo, Maravi Express yamvetsedwa motere. Izi akuti zinachitika kumapeto a sabata yatha pa malo ena omwera mowa omwe amatchuka kuti Desert ku Bangwe mumzinda wa Blantyre. Malinga ndi kunena kwa mkulu wina yemwe amakhala ku Masala wotchedwa Bladson Phimba , mkuluyo akuti wakhala akupapira mowa kwambiri ndipo patsikulo akuti atangoweluka ku ganyu yake anaganiza zokamwa mowa wachilendowo ndi anzake. “Pambuyo pokhuta kwambiri iye anauyamba…

Read More

Asesa Katundu Yense Atapezelera Mamuna Wake Akuchita Za Dama ndi Chibwenzi Likuswa Mtengo

Mayi wina ku Nguludi m’boma la la Chiradzulu akuti masiku apitawa anasesa ndi kunyamula katundu yense wa mnyumba ulendo kumudzi kwawo atapezelera mamuna wake akuchita za dama ndi mayi wina woyendayenda dzuwa likuswa mtengo m’matolo. Malinga ndi kunena kwa bambo Alick Phinifolo omwe amachita geni yowoda nkhuku nkumagulitsa ku Limbe, nkhaniyi yati maiyo wakhala akukayikila mayendedwe a mamuna wakeyo atatsinidwa khutu kuti anthu akhala akuwona ndi kamtsikana kena koyendayenda koma mkuluyu akuti wakhala akukanitsitsa kwantu wa galu akamufunsa. Ndiye…

Read More

Amangililidwa M’mitengo ku Manda Kamba ka Chibwana cha Nchombo Lende

Amuna atatu posachedwapa akuti anamangililidwa m’mitengo ku manda m’boma la Phalombe kamba koledzera mosachita bwino pamene mwambo wa maliro unali mkati kumeneko. Malinga ndi bambo Mark Phinifolo omwe anafotokozera Maravi Express za nkhaniyi, anthu anali odabwa pamene anyamata ena omwe ndi achibale a malemuyo omwe amakhala mumzinda wa Blantyre akuti anakhuta kwambiri bibida pamene anthu komanso a mpingo amakhazika zovutazo pa siwapo. Ndipo kutacha makosanawo akuti sanalekere pomwepo koma anapitilizabe kuudadanya mowa kenaka anapita kukakhala nawo pa mwambo wa…

Read More

Zigandanga ziphedwa kamba kofuna KUbera Anthu

Malipoti omwe afikila Maravi Express akuti anamalira pa Tauni agagada ndi kupha anthu atatu omwe amawaganizira kuti ndi mbava. Izitu zachitika mu limodzi la maboma a mdziko lino mchigawo chakumwera. Malinga ndi kunena kwa mayi Eneya, mbavazo zinagagadidwa atazigwira pamene zimafuna kuba pa ina mwa sitolo za pamalopo. Apolisi atsimikiza za nkhaniyi ndipo auza anthu kuti azipita mwamsanga kukanena ku polisiko ngati ataganizira munthu kuti ndi tsinzinantole. Miyezi yapitayi apolisi akhwimitsa chitetezo m’maboma ambiri mdziko muno. Nawonso anthu sakulola…

Read More

Anjatidwa Pambuyo Pogagada Ndi Kupha Mkazi Wake ndi Mpini

Mkulu wina ku Makanjira m’boma la Mangochi amuthira zingwe ati kamba koti anagagada ndi kupha mkazi wake ku Makanjira m’boma la Mangochi kamba ka nsanje, Mraravi Express yamvetsedwa motere. Malinga ndi kunena kwa bambo Phiri omwe anaonekera ku ofesi ya Maravi Express kudzatsindika za nkhaniyi, mkuluyo akuti wakhala akukayikira ndi mayendedwe a mkazi wakeyo. Tsiku lina mkuluyo atachoka pakhomopo akuti anatsinidwa khutu ndi anzake kuti adawona mkazi wakeyo ali ndi njonda ina ndipo izi zinamukwiyitsa kwambiri ndipo sanachedwe koma…

Read More