Apalana Ubwenzi Wamseli ndi Mayi Komanso Mwana

Mkulu wina ku Nancholi mumzinda wa Blantyre akuti wakhala akuyenda ndi mayi wina kuphatikizanso wana wake wamkazi woyamba Maravi Express yamvetsedwa motere. Malinga ndi kunena kwa bambo wina yemwenso amakhala ku Nancholi komweko wati mkuluyo yemwe ali ndi banja lake lokhazikika anapalana unbwenzi wamseli ndi mayi wina wochita bizinesi yemwenso ali pa banja. Ubwenziwo akuti wakhala zaka zingapo kamba koti mamuna wa maiyo anapita mdziko la South Africa kukagwira ntchito zaka zingapo zapitazo. Koma kenaka mkuluyo akuti anayamba kudekhera…

Read More

Akozedwa Atapapira Mowa pa Mwambo wa Chikwati

Zina ukamva amati kamba anga mwala anthuni. Mnyamata wina yemwe amapanga bizinesi ya zitsulo za njinga ku Chirimba mumzinda wa Blantyre akuyenda wera wera ngati nkhuku ya Chitopa kamba koti anakozedwa mu holo pa mwambo wa Chikwati cha mlongo wake sabata yatha. Malinga ndi kunena kwa m’modzi mwa anthu omwe anawonelera mwambowo a Justin Kanje omwe amakhala ku Chilomoni, zinthu zonse pa tsikulo zinayamba bwino pamene ukwatiwo unadalitsidwa ku limodzi mwa matchalichi kumeneko. Kenaka itatha nthawi ya chakudya chikwaticho…

Read More

Mphunsitsi Wankulu Asambitsidwa Ndi Zibagera ku Bangwe

Mphunzitsi wankulu wa pa sukulu ina yapulaimale ku Bangwe masiku apitawa anasambitsidwa ndi zibagera zomwe zinavumbwa kuchokera kwa makolo omwe anakwiya kamba koti m’modzi mwa aphunzitsi anamenya ndi kukomola mwana wasukulu. Malinga ndi malipoti omwe afikila Maravi Express, m’modzi mwa aphunzitsi kumeneko anamenya ndi kukomola mwana wachichepere, chinthu chomwe chinapangitsa makolo komanso anthu ena omwe amagulitsa katundu wosiyanasiyana kumeneko kulowa mumpanda wa sukuluyo momwe anafuna kumva bwino lomwe chomwe chinachitika. Nawonso ophunzira sanaimve koma kutseka msewu kwinako akuyimba nyimbo…

Read More

Chimbalangondo Chiwotchedwa ku Bangwe Kamba kakuba ma Babu

Koma zinazi munthu ukamva sungazimvetsetse kamba ka zinthu zomwe zachitika masiku apitawa ku Mbayani mtaunishipi ya Bangwemumzinda otchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre. Bambo wina kumeneko wataya moyo wake atamupeza akuchotsa ma babu pa ina mwa nyumba zamumpanda kumeneko. Malipoti omwe afikila Maravi Express akuti mkuluyo wakhala akuba zinthu zina ndi zina kuphatikizapo mbaula ndi mapoto. Ndiye patsiku lake la 40 litakwana iye anaganiza zokwera mpanda nkuyamba kuchotsa ma babu a nyumbayo. Koma alonda atamuona anayamba kumuthamangitsa ndipo kenaka…

Read More

Amwalira ndi Mowa Wachilendo Kamba Kosadyera

Mkulu wina yemwe anali wa zaka zakubadwa makumi asanu ndi mphambu imodzi (60) akuti masiku apitawa anataya moyo wake kamba komwa mowa wina wofanana ndi madzi koma osadyera. Malemuyo yemwe dzina lake ndi Kalata Mdukamwera akuti anali mbiyang’ambe kwambiri ndipo ankakhalira moyo wake wa tsiku ndi tsiku pogwira ganyu kapena kuti zija ena akuti magobo masiku ano. Anafotokozera atolankhani nkhaniyi ndi m’modzi mwa abale a malemuyo a Yosofati Chilooko. Patsikulo akuti malemuyo anauza abale ake kuti akupita ku mudzi…

Read More

Mphunzitsi Amenya ndi Kukomola Ophunzira

Anthu ena akhala akudandaula kunkhani ya nkhanza zomwe aphunzitsi ena akhala akuchitira ophunzira msukulu zina mdziko muno. Izitu zatsimikizika pamene mphunzitsi wina anamenya ndi kukomola ophunzira masiku apitawa. Nkhaniyi inachitika pa sukulu ya pulayimale ya Makata mtaunishipi ya Ndirande mumzinda wa Blantyre. Malinga ndi kunena kwa bambo Banda omwe anawona izi zikuchitika maso ndi maso, mphunzitsiyo yemwe amaphunzitsa mu kalasi 7 pasukulupo anawona ophunzira wa Kalasi 4 akukoza pa mpanda. Kenaka mphunzitsiyo anazembera mwanayo ndi kumukuntha mbama yomwe anagwa…

Read More

Akhakhathana Ndi Zikwanje Kamba Kolimbirana Malire

Kunali chindeu cha ndiwe yani makamaka chokhakhathana ndi zikwanje pakati pa maanja awiri omwe amakhala pa mapuloti ena kwa Nkwate ku Machinjiri mumzinda wa Blantyre, Maravi Express yamvetsedwa motere. Malinga ndi kunena kwa mayi wina yemwe anangodzitchula kuti ndi a Nansefu omwe amakhalanso pafupi ndi maanjawo, izi akuti zinayambika pamene chimbudzi cha banja lina kumeneko chinadzadza ndipo analemba aganyu omwe anayamba kukumba china m’malire ndi puloti inayo. Koma poona izi mayi wa banja linalo anatchayira thenifolo mamuna wake nkumuuza…

Read More

Athamangitsa Mkazi Wake Kamba Komulalatira Ali Mchipatala

Mkulu wina ku Lirangwe akuti wathetsa banja lake kamba koti mkazi wake sanamulankhule bwino pamene anali mchipatala Maravi Express yamvetsedwa motere. Malinga ndi kunena kwa mkulu wina yemwe amacheza ndi bamboyo, nkhaniyi yati mkuluyo anayamba kudwala m’mimba ndipo anagonekedwa pa Chipatala cha Mlambe masiku apitawa. Koma akuti mkazi wakeyo amanyinyilika zokagoneka matendawo mchipatalamo ndipo achemwali a mamunayo ndiwo amadwazika matendawo. Chomwe chinakwiyitsa kwambiri mamunayo kuti athetse banjalo nchakuti maiyo anamulankhula kuti ‘Inutu m’mene munaliri muja tinakangoika basi.’ Pamene amalanhula…

Read More

Akwaya Agenda Nyumba Ya M’busa Wawo Patagwa Zovuta

Achinyamata a gulu lina loyimba nyimbo za ambuye akuti masiku apitawa anadabwitsa anthu pamene anakuwiza komanso kugenda nyumba ya m’busa wa pa mpingopo ati kamba koti sanafike pa maliro a m’modzi mwa oyimbao yemwe anatisiya atadwala kanthawi kochepa. Malinga ndi kunena kwa mkhristu m’modzi pa mpingowo, woyimbayo atamwalira akulu a mpingo ku dera limenelo sanachedwe koma kuthamangila kwa Abusa kukawafotokozera za zovutazo. Koma akuti pasanapite maola angapo, akulu ampingo ena anapitanso kwa m’busayo ndi kukamuuza kuti malirowo samayenera kuyimbilidwa…

Read More

Awumbuzana Molapitsa Kamba kolimbirana mamuna

Asungwana ena woyendayenda kwa Manje mumzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre kumapeto a sabata yatha akuti anakwapulana molapitsa kamba kolimbirana njonda ina yomwe imachita bizinezi yogulitsa nsomba mumsika wa Limbe. Malinga ndi kunena kwa mkulu wina yemwe anawona izi zikuchitika maso ndi maso, njondayo yakhala ili pa ubwenzi wamseli ndi m’modzi mwa amayiwo kwa zaka zingapo ndipo akafika pa mabala a kumeneko saumila kunkhani yogula zakumwa zaukali. Koma masiku apitawa akuti njondayo inapalananso ubwenzi ndi msungwana wina yemwe…

Read More