Mwana Aseweretsa Njoka koma Osalumidwa

Anthu ena kwa Likoswe m’boma la Chiladzulu akuti anazizwa kamba koti mwana anapezeka akuseweretsa njoka koma sinamulume, Maravi Express yamvetsedwa motere. Malinga ndi kunena kwa mkulu wina yemwe amachita geni yogulitsa nkhuku pa msika wina kumeneko, banjalo patsikulo linapita kumunda kukapalira Chimanga pamodzi ndi anthu ena omwe anawalemba ganyu. Atafika kumundako maiyo akuti anakhazika mwana wake wachichepere pansi pa mtengo wa Mango osadziwa kuti chapafupi panali njokayo. Kenaka kupalira kuli mkati mai uja anaganiza zokazonda mwanayo pansi pa mtengo…

Read More

Afafanthidwa Modetsa Nkhawa Atapezeka mu Nyumba Yogona Alendo ndi Mamuna wa Mwini

Koma asungwana enawa sadzamva ku nkhani yogona ndi amuna ayeni. Msungwana wina woyendayenda ku Bangwe mumzinda wa Blantyre akuti masiku a chisangalalo cha khisimasi ndi chaka chatsopano anawona zakuda m’malo mokonwelera nyengoyi. Nkhaniyi yati pamene anthu amakondwera kutsanzikana ndi chaka cha 2016 m’madera ambiri mdziko muno maka kumbali yoti ambuye mulungu watisunga ndi moyo chaka chimenechi, nawonso asungwana ambiri amachiwona ichi ngati chinthu cha mtengo wa patali kuti agonane ndi amuna a eni m’malo ogona alendo osiyana siyana kuti…

Read More

Wamisala Adabwitsa Anthu Atathawitsa njinga Kenaka Nkubwelera Nayo Patapita Maola Angapo

Athu ochita malonda pa msika wina mb’oma lotchuka kunkhani yolima mbeu ya tiyi ku Thyolo akuti anafa ndi phwete pamene wamisala wina anathawitsa njinga ya mkulu wina yemwe panthawiyo amataya madzi . Nkhaniyi yati mkuluyo yemwe amagwira ntchito pa imodzi mwa mafakitale kumeneko anayimitsa njinga yake nkulowa mu tiyimo kuti ataye madzi ndipo asanatero anauza makosana ena omwe amasewera bawo pakhonde la wokala ina kuti amuyang’anire. Koma akuti atangoyimika njingayo, wamisala wina yemwe amazungulira m’misika kumeneko anavumbuluka ngati kamvuluvulu…

Read More

Agamulidwa Zaka Khumi ndi Ziwiri Ku Jere Kamba Kogwililira Ana Okhala Ake Omwe

Koma anthu ena ayi ndithu. Khothi la majisitireti loyamba la m’boma la Kasungu posachedwapa lidalamula njonda ina ya zaka 29 kuti ikakhale kundende kwa zaka khumi ndi ziwiri atapezeka olakwa pa mlandu ogwililira ana ake awiri. Anawo akuti ndi a zaka zisanu ndi ziwiri (7) komanso zisanu ndi zinayi (9). Mkuluyo yemwe sanatchulidwe dzina pofuna chitetezo anamunjata pa 23 Novembala kamba ka mchitidwewo womwe akuti wakhala akuchita kwa zaka ziwiri tsopano. Izi akuti zinaululika kamba koti mwana wa zaka…

Read More

Agwetsa Kachisi Kamba Kosamvana Maganizo Kunkhani Ya za Chuma

Dzikoli kaya likulowera kuti anthuni? Akhristu pa mpingo wina kwa Ntopwa mtaunishipi ya Bangwe munzinga wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre masiku apitawa akuti anagwetsa Kachisi kamba kosamvana maganizo ndi m’mene akuluakulu akhala akuyendetsela ndondomeko ya za chuma. Malinga ndi kunena kwa a James Milanzi omwe amakhala kwa Ntopwako pafupi ndi tchalitchilo, akhristuwo akuti akhala akudabwa ndi m’mene chuma chakhala chikuyendela pa mpingowo maka popeza ntchito yomanga kachisiyo inali ikupitilirabe. “Akhristuwo akuti akhala akupereka moolowa manja kwa zaka zapitazi…

Read More

Avulazidwa Molapitsa Kamba Kopezeka Kuchipinda Mnyumba ya Mwini

Mkulu wina ku Bangwe mumzinda wa Blantyre masiku apitawa anaphopholedwa molapitsa kamba koti anapezeka kuchipinda cha nyumba ina yoyandikana nayo ali gonee pa kama. Malinga ndi omwe atofotokozera Maravi Express nkhaniyi, mkuluyo akuti wakhala ali paubwenzi wamseli ndi mkazi wa mzake wa nyumba yoyandikana nayo ndipo awiriwo akhala akumakumana mnyumbamo mwini mkaziyo akapita kuntchito ya ugadi mtauni ya Limbe. Anthu akuti akhala akunon’goneza gadiyo za nkhaniyi koma iye samakhulupilira kuti izi zimachitikadi ati kamba koti akhala kupapila limodzi mowa…

Read More

Mayi Wina Aphopholedwa ndi kuvulidwa Kamba kochitira Nsanje Mamuna wa Mwini

Mayi wina ku Bangwe mumzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre masiku apitawa anawona ngati ku tulo pamene anaphopholedwa molapitsa ati kamba kochita nsanje ndi mwini mamuna. Nkhaniyi ikuti maiyo wakhala akuyenda ndi mamuna wa mwini kwa zaka zingapo koma wakhala akupanga izi ndi izi kuti alande mwini banjalo yemwe amangwira ntchito ngati dotolo pa chipatala china kumeneko. Kenaka amayi awiriwo akuti atakumana pa malo okwelera basi kunali kuphopholana osati masewera koma mwini banjalo mothandizana ndi anzake omwe analowelera…

Read More

Azikhweza Pambuyo podziwa kuti mkazi wake ali ndi Mamuna wina

Mkulu wina ku Ndirande Makata posachedwapa akuti anazimangilira kamba koti anazindikila kuti mkazi wake anapalana ubwenzi wamseli ndi njonda ina yomwe imayitanira minibasi pa msika waukulu kumeneko. Malipoti omwe afikila Maravi Express ati maiyo pa tsikulo sanagone kunyumba kwake koma anakagona kwa mamuna wakubayo. Kutacha maiyo anapita kunyumbako ndipo mamunayo atamufunsa komwe anali iye ananenetsa kuti anagona kwa abale ake kamba koti kunja kunamudela. Apa akuti awiriwo sanamvane Chichewa ndipo kenaka maiyo akuti anauyamba ulendo wopitanso kukagona kwa njonda…

Read More

Akhapa Bambo wa Mwana Wofuna Kugwililidwa Poyesa kuti Ndiye Amafuna Kugwilira

Zina ukamva kamba anga mwala anthuni. Anthu okhala mtaunishipi ya Zingwangwa mumzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre anazidwa komanso kuchita nthumazi kamba ka nkhani yomwe yafikila zikuchitika pozachedwapa. Malipoti ati mkulu wina yemwe amachita bizinezi yowonetsa kanema mumsikawo masiku apitawa anayitanila mwana wosakwana zaka khumi mu nyumba yomwe amawonetsela kanemayo momwe anayamba kumugwilagwila pofuna kumugwililira. Koma amayi ena ogulitsa nkhuni pafupi ndi nyumbayo anadabwa poona kuti chitseko cha nyumbayo chinakhomedwa. Amayiwo anafotokozela anyamata ena omwenso amachita geni pa…

Read More

Akomoledwa Atapezeleledwa Akuchita za Dama ndi Mamuna wa Mwini

Msungwana wina woyendayenda ku Makhetha mumzinda wa Blantyre akuti masiku apitawa anaumbuzidwa mpakana kukomoka atamupezelera akuchita za dama ndi mamuna wa mwini. Mayi Falawo omwe anaona izi maso ndi maso anafotokozera Maravi Express kuti msungwanayo wakhala akuchita mchitidwe omadekhela maso ndi kumagona ndi amuna ayeni kwa nthawi yaitali m’mabala osiyanasiyana kumeneko. Ndiye paja akulu amati ukatambatamba udziyamba wayang’ana kunyanja chifukwa choti kungakuchere, tsiku lake lachiweluzo linafika pamene anakumana ndi zokhoma. Nkhaniyi yati mkulu wachimasomasoyo anapita kukapapila mowa pa bala…

Read More