Apezeleredwa Akuchita za Dama ndi Msungwana Wokolopa

Wolemba: Richard Chinansi Banja lina kwa Nkwate mdera la mfumu yaikulu Machiniri mumzinda wa Blantyre akuti lagawanapo zida kamba koti mayi wa mnyumbamo anapezelera mamuna wake akuchita za dama ndi msungwana yemwe anamulemba ntchito yokonza mnyumbamo. Malinga ndi mayi Christina Chirwa omwe amakhala pafupi ndi nyumba yomwe kwachitikira izi, iwo anafotokozera Maravi Express kuti banjalo lomwe linadalitsidwa pa mpingo wina kumeneko chaka chatha linadalitsika ndi mphatso ya mwana wamwamuna miyezi ingapo yapitayi. Choncho izi zitatero awiriwo anagwirizana zoti alembe…

Read More

Mkulu Wampingo Apezeleledwa Akuchita za Dama ndi Mkazi Wamwini

Wolemba:Richard Chinansi Mkulu wa mpingo wa imodzi yomwe yangoti m’bwee m’madera ambiri mziko muno ku Chilaweni m’boma la Blantyre akuti akuyenda mozolika ngati nkhuku ya Chitopa pamene anamupezelera akuchita za dama ndi mkazi wa mzake yemwe anali ponda apa nanenso ndiponde apa ndi mkazi wake. Maanjawo akuti amakhala nyumba zoyandikana komweko ku Chilaweni. Malinga ndi kunena kwa a Fanuel Banda omwe amakhala pafupi ndi komwe kunachitikira nkhaniyi, mwini mamunayo akuti wakhala akudabwa ndi mayendedwe a mamuna wakeyo makamaka iye…

Read More

Afafanthidwa Modetsa Nkhawa Kamba Kochita za Dama ndi Mkazi wa Mwini

Wolemba: Richard Chinansi Mamuna wina wa chimasomaso kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo akuti masiku apitawa anafafanthidwa modetsa nkhawa pamene anamupezelera akuchita za dama ndi mkazi wa mwini. Malinga ndi kunena kwa bambo Gama omwe amachita geni ya Kabichi pamsika wa Bvumbwe, nkhaniyi yati mwini mkaziyo wakhala akukayikira za mayendedwe a mkazi wake maka-maka akapita kukachita geni yake ya Nkhuku pamsika omwewo wa Bvumbwe. Anthu enanso akufuna kwabwino akuti akhala akutsina khutu mamunayo kuti mkazi wake akuyenda mwa mseli ndi…

Read More

Mbava ipezeka ili Mbulanda pa Denga

Wolemba: Richard Chinansi Zina ukamva kamba anga mwala anthuni. Munthu wina yemwe akumuganizila kuti ankafuna kuthyola ndi kuba pa nyumba ya mkulu wina kwa Gayesi mumzinda wa Blantyre akuti anapezeka ali pa denga la nyumbayo koma ali chinochino. Nkhaniyi yati mwini nyumbayo anadabwa pamene chitseko chake chinkamveka ngati pali munthu wina yemwe amalimbana nacho kuti athyole. Izi zili choncho mwini nyumbayo akuti anayamba kukuwa pofuna kuti anthu oyandikana nawo adzuke ndi kumuthandiza pa zomwe zimachitikazo. Atamva mkuwowo mbavayo akuti…

Read More

Mayi Waulemu Wake Amupezelera Akuchita Za Dama ndi Mnyamata Waganyu

Mayi wina ku Makhetha mumzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre akuti masiku apitawa anawona ngati kutulo pamene anamupezelera akuchita za dama ndi mnyamata wina yemwe anamulemba ganyu yokolora chimanga ku munda . Izitu akuti zinachitika dzuwa litangopendeka pamene anthu masiku ano ali kalikiliki kukolora mbeu zawo. Malinga ndi kunena kwa a Anthony Chisasa omwe ayandikana minda ndi wa banja la mayi wachimasomasoyo, iwo anati mamuna wake yemwe amakhala mdziko la South Africa wakhala akutumiza ndalama kwa mkazi wakeyo…

Read More

Mbava Yokuba Maungu Iwona Mbwadza Atayiwumbuza Ngati Yagundidwa ndi Sitima

Pamene anthu ali kalikiliki m’madera ambiri mdziko muno kukolora chimanga komanso mbeu zina monga maungu ndi nkhaka, mkulu wina anachitenga ichi ngati chinthu cha mwayi kuti nayenso akolore pamene sanalime. Maravi Express yamvetsedwa kuti mkulu wina kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo wakhala akupita ku minda ya anthu osiyanasiyana kwa mfumu yaing’ono Chiwaya komwe wakhala akuba maungu nkumakawagulitsa mu msika wa Limbe kangapo konse. Anthu ena ndiwo akuti anadabwa ndi mkuluyu popeza tsiku ndi tsiku amamuona pa malo ena okwelera…

Read More

Chikopa cha Galu ndi mutu zipezeka M’bali mwa Mtsinje wa Limbe

Koma maidya idyawa nthawi zina makamaka anthu okhuta mowa amatha kudya zosadya ndithu. Masiku apitawa akuti anthu ena omwe amalima madimba awo m’bali mwa mtsinje wa Limbe anapeza Chikopa ndi mutu wagalu pathengo lina loyandikana ndi msika waukulu wa Limbe. Anthu amenewa akuti anayitanizana ndipo nawonso mavenda anakhamukila kukawona zinthu zimenezi. Malinga ndi kunena kwa a Pitala Gama, anthuwo akuti galuyo akukhala ngati anagundidwa ndi galimoto ndipo palibe chikayikitso kuti anachita kusendedwa ndi munthu wina wankhanza yemwe nkutheka kuti…

Read More

Mnyamata Adabwitsa abale ake atapezeka akukodzera m’beseni la Madzi

Zinthu zina abale kamba anga mwala anthuni. Banja lina ku Ndirande mumzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre lidawona ngati malodza pamene mwana wawo wa mamuna anamupezelera akukodzera m’beseni ya madzi yomwe anaiyika pakhonde pofuna kupeza madzi a mvula. Izitu zinachitika ku dera lomwe limatchuka kuti Zambia mtaunishipi imeneyi ya Ndirande masiku apitawa. Malinga ndi kunena kwa mkulu wina yemwe anangodzitchula dzina kuti Banda, mnyamatayo patsikulo anakhuta mowa wina wofanana ndi madzi ndipo mvula itayamba anapita kunyumba nkukagona. Kenaka…

Read More

Ayimitsa Anthu Mitu Atapezeka Akujambulitsa Zithunzi Ali Mbulanda

Anthu ena omwe amakhala ku Chitawira mumzinda wa Blantyre masiku apitawa akuti anayima mitu pamene msungwana wina yemwe akumukhulupilira kuti ndi woyendayenda anali pa chi ntchito chotoletsa zithunzi kwa mkulu wina mu malo ochitira macheza aja amatchuka kuti Njamba Park dzuwa liri pa liwombo. Malinga ndi kunena kwa bambo Emmanuel Banda omwe anawona izi zikuchitika maso ndi maso, iwo anauza Maravi Express kuti msungwanayo anafika pa malowo ndi chikwama chake nkukhala pansi pa mtengo kuyembekezera mkulu wotola zithunziyo. Ndipo…

Read More

Akulu a mpingo Agawana Ndalama za Mpingo Nkukagulira Zofuna Kumtima Kwawo

Zina ukamva anthuni kamba anga mwala akulu anatero. Anthu kwa Gwaza m’boma la Balaka akuti masiku apitawa anayima mitu pamene zinamveka kuti akuluakulu a mpingo wina anagawana ndalama zomwe bungwe lina linapereka pa mpingowo nkukagulira zofuna zawo. Malinga ndi kunena kwa mayi Nadimba omwe amakhala pafupi ndi tchalichilo, akhristu kumeneko akhala akuchitira mapemphero awo mkachisakasa kwa zaka zingapo ndipo anagwilizana zoti amange kachisi watsopano. Pa ichi iwo anagwilizana zolembera kalata zingapo ku mabungwe a kunja omwe amathandiza mipingo munjira…

Read More