Adabwitsa Anthu atavina mwa kaso ndi Kabuduka wa Mkati Yekha

Pamene anthu ali kalikiliki m’madera osiyanasiyana a dziko lino kukonzekera chisangalalo cha Khisimesi cha chaka chino nalonso tsamba la zikuchitika pa Maravi Express likunka limwaza maso ake ndi cholinga chofuna kukudziwitsani nkhani zochitisa chidwi zomwe zayamba kale kuchitika padakali pano.
Anthu ambiri omwe amachita bizinezi zosiyana siyana pa msika wa Bvumbwe nawonso anayima mitu pamene bambo wina anavina ndi msungwana wina ndi kugwetserana pansi yemwe anavula zovala zake nkusala ndi kabudula wa mkati yekha kwinaku ati kamba ka nyimbo ina yomwe inaphulika pa malo ena omwela mowa kumeneko.
Malinga ndi kunena kwa mayi Benito omwe amagulitsa phwetekere pa msika wa Bvumbwe, zonse zinayamba pamene imodzi mwa makampani odziwika ndi kuphika mowa wa masese mdziko muno inakonzera makasitomala ake a kwa Bvumbwe dansi ya dzaoneni (Disco) ngati imodzi mwa njira yowathokoza kamba koyigula mowa mchaka chimene chikupita ku malichelichechi cha 2017.
Iwo anafotokozera zikuchitika kuti dansiyo inayamba cha kum’mawa ndipo mbiya ng’ambe zomwe zimachita geni pa msika wa Bvumbwe kuphatikizapo atsikana oyendayenda anachiwona ngati chinthu cha nzeru kukhamukira ku malowo kukapapira mowa komanso kugwedeza matupi awo ngati imodzi mwa njira yokonzekera khisimesi pa 25 Disembala.
Dansiyo akuti inakoma kwambiri pamene anthu ambiri anakhuta mowa ndipo nawonso asungwana oyendayenda sadachitire mwina koma kulowa m’bwalo kuvina mwa kathithi nyimbo zomwe anyamata a kampaniyo anaphulitsa kudzera ku choyimba chawo chomwe chimamveka ngakhale ku malo ena ozungulira msikawo.
Koma akuti izi zili dere, bambo wina yemwe anthu akumuganizira kuti anamwa kachasu anakwapatirana ndi msungwana wina nkuyamba kuvina ndipo kenaka msungwana uja anadabwitsa anthu pamene anavula bulauzi ndi siketi yake nkusala ndi kabudula wa mkati yekha nkukokera bamboyo pansi.
Izi akuti zinapangitsa anthu ambiri a malonda kukhamukira ku malo a dansiyo kukachemelera sitepe yachilendoyo koma zili choncho amayi ena odula mowa akuti anaduduluza msungwanayo nkumuthamangitsa pa malowo koma ali zandizandi osadziwa njira ya kwawo kwinaku akukuwidwa ndi khamu la anthulo.
Dansiyo inapitilira mpakana madzulo monga mwachikonzero ndipo m’mene zonse zimatha nkuti mbiya ng’ambe zambiri ziri thaphya kamba ka ululu wa mowawo.