Ayenda ndi Kabudula Wamkati Yekha Kamba Kolephera Kumaliza Ndime

Mkulu wina anawona ngati za kutulo masiku apitawa pamene anavulidwa zovala zonse nkusala ndi kabudula wamkati yekha pa malo ena omwela mowa ndi msungwana wina yemwe anamulemba ganyu yoti amuthandize kulima munda wake omwe uli pa mudzi wa William mdera la mfumu yaikulu Bvumbwe m’boma la Thyolo.
Mayi Naomi Benadi omwe anawona izi zikuchitika maso ndi maso anafotokoza kuti mkuluyo wakhala akuchita khalidwe limeneli kwa nthawi yaitali lomanka alandila ndalama zonse akafunsa ganyu koma akangoyamba ndime samaliza popeza amathawa nkupita kukafunsilanso ganyu kwina.
Ndiye patsikulo akuti msungwanayo yemwe wangofika kumene pa lendi m’mudzimo anapeza munda woti alime kamba ka mvula yomwe yayamba kugwa bwino m’madera ambiri mdziko muno ndipo kenaka anauza ana kuti amufunire munthu waganyu kuti akalime kumundako.
Mkuluyo atamva za nkhaniyi akuti anathamangila kunyumba kwa msungwanayo komwe anagwirizana za malipiro a ntchitoyo.
Kamba kofunisitsa kuthana ndi ntchito ya kumundako mwachangu msungwanayo akuti anapelekeratu ndalama zonse kwa kapsyaliyo kuti akayambe ntchitoyo.
Mkuluyo akuti atangoyamba kulima mizere ingapo anamva choyimba pa malo ena omwera mowa ndipo sadaupeze mtima koma kuthawa ganyuyo kuti akasukuluze kukhosi ndi anzake ena omwe wakhala akumwa nawo mowa wina wofanana ndi madzi masiku apitawa. Asanafike kumowako mkuluyo akuti anakumana ndi anyamata ena omwe amachita geni ya zovala pa msika wa Bvumbwe ndipo anamusatsa buluku ndi Malaya zomwe iye anagula mozanenelera ati cholinga akawoneke kuti watchena kumowako pakati pa anzake.
Atafika mkuluyo akuti anasungitsa khasu kwa mwini bala nkuyitanitsa zigubu ziwiri za mowawo ndipo anayamba kupapila ndi anzakewo ngati kulibe mawa mpakana kuledzeleratu. Kenaka mkuluyo akuti anayamba kuvina ndi anzake aja osadziwa kuti msungwana uja wayendera kale kumunda kuja ndipo anapeza kuti palibe chomwe chinachitika.
Kenaka msungwanayo atafufuza za mkuluyo akuti anthu anamuuza kuti ali thaphya pa malo omwera mowawo ndipo mosataya nthawi anapanga hayala njinga ya kabaza ulendo komweko. Msungwanayo yemwe akuti ndi wadzitho ngati mwamuna akuti sanachite mantha konse ndi anthu omwe anali pa mowapo koma anangoti gwiru pakhosi mkuluyo namuuza kuti amubwezere ndalama .
Apa mkuluyo anayesetsa kulimba-limba koma msungwanayo m’maso muli gwaa anamukokera kunja kwa mpanda wa malo omwela mowawo kenaka nkumuvula zovala zomwe zimaonekadi kuti ndi zatsopano.
Msungwanayo atayang’ana m’matumba a zovalazo akuti sanalipeze ngakhale loboola ndipo kenaka anakwera njinga ija ulendo ndi zovala zija nkusiya khwimbi la anthu likuyimba mkulu uja nyimbo zochititsa manyazi kwinaku ali zandi-zandi ulendo wa kunyumba kwake.