Apezeleredwa Akuchita za Dama ndi Msungwana Wokolopa

Wolemba: Richard Chinansi

Banja lina kwa Nkwate mdera la mfumu yaikulu Machiniri mumzinda wa Blantyre akuti lagawanapo zida kamba koti mayi wa mnyumbamo anapezelera mamuna wake akuchita za dama ndi msungwana yemwe anamulemba ntchito yokonza mnyumbamo.
Malinga ndi mayi Christina Chirwa omwe amakhala pafupi ndi nyumba yomwe kwachitikira izi, iwo anafotokozera Maravi Express kuti banjalo lomwe linadalitsidwa pa mpingo wina kumeneko chaka chatha linadalitsika ndi mphatso ya mwana wamwamuna miyezi ingapo yapitayi.
Choncho izi zitatero awiriwo anagwirizana zoti alembe msungwana woti azithandiza zina ndi zina za pakhomopo kamba kotinso onse awiri ali pa ntchito m’makampani ena omwe ali mumzinda omwewo wa Blantyre.
Kenaka maiyo akuti anayamba kudabwa ndi magwiridwe a ntchito a msungwanayo omwe amakhala onyinyilika kusiyana ndi poyamba komanso kangapo konse amabweza moto kwa mwini khomolo akamulankhula akalakwitsa pena pake.
Izi akuti zakhala zikuchitika kwa nthawi ndithu koma maiyo akadandaulira mamuna wakeyo za machitidwe a msungwanayo, iye samachitapo kanthu ngakhale kuonetsa chidwi ati popeza anali wochokera ku banja lina la achibale awo kumudzi m’boma la Chiradzulu.
Koma paja akulu amati ukatambatamba udziyamba kaye wayang’ana kunyanja kamba koti kunja kungakuchere, nkhaniyi ikuti anthu ozungulira pa pulotiyo anayambanso kudabwa ndi bamboyo kamba koti maiyo akachoka iye amatengana ndi wantchitoyo pa galimoto kumanka m’madera osiyanasiyana.
“Tsiku lina bamboyo akuti anauza mkazi wakeyo kuti sapita ku ntchito kamba koti samamva bwino mthupi ndipo panafunika kupita ku chipatala. Maiyo akuti sanavute koma kuuyala ulendo wa kuntchito kwake.
“Atafika kuntchitoko akuti abwana ake anamufunsa za cheke chomwe anamutuma kuti akatenge dzulo lake ndipo iye ananena kuti anachiyiwala kunyumba ndipo posakhalitsa bwanayo akuti anauza dalaivala wa pakampanipo kuti aperekeze maiyo kuti akatenge chekecho kunyumbako,” anafotokoza motere mayi Chirwa.
Iwo anapitilira nkuuza Maravi Express kuti atangofika kunyumbako maiyo sanalabadile zogogoda koma anangofikira ku chipinda kuti akatenge chekecho koma ngati kutulo anayima mutu pamene anapezelera mamuna wakeyo ali kalikiliki kuchita za dama ndi msungwana wantchitoyo.
Apa maiyo sanachitire mwina koma kuumbuza wantchitoyo ali chinochino ndipo apa mamunayo akuti anapeza mpata wongonyamula kachikwama ka zovala zake zina nkuyamba kuthawa kudzera njira zamadulira ndipo padakali pano sakudziwika komwe ali ngakhalenso kuntchito sakufikako.
Anthu ena achifundo ozungulira nyumbayo akuti ndiwo analesetsa wantchitoyo kamba koti maiyo anamuvulaza kosaneneka ngati kuti wagundidwa ndi sitima.
Msungwanayo akuti anamuthawitsa atangovala ka chitenje komwe mayi wina anamupatsa ndipo maiyo wanenetsa kuti sangasinthe maganizo oti banjalo laumapo ngakhale ena anamulangiza kuti akafikitse nkhaniyi kwa ankhoswe.