Mkulu Wampingo Apezeleledwa Akuchita za Dama ndi Mkazi Wamwini

Wolemba:Richard Chinansi
Mkulu wa mpingo wa imodzi yomwe yangoti m’bwee m’madera ambiri mziko muno ku Chilaweni m’boma la Blantyre akuti akuyenda mozolika ngati nkhuku ya Chitopa pamene anamupezelera akuchita za dama ndi mkazi wa mzake yemwe anali ponda apa nanenso ndiponde apa ndi mkazi wake. Maanjawo akuti amakhala nyumba zoyandikana komweko ku Chilaweni.
Malinga ndi kunena kwa a Fanuel Banda omwe amakhala pafupi ndi komwe kunachitikira nkhaniyi, mwini mamunayo akuti wakhala akudabwa ndi mayendedwe a mamuna wakeyo makamaka iye akapita kumudzi kwawo kwa Jali kukawona za kumunda.
Ndiye patsikulo akuti mayi wa mnyumbamo anatsanzika kuti akupita kumudzi kuti akatenge Nandolo ndipo bamboyo sanavute koma kupereka ndalama yoti akwelere basi ndipo awiriwo anaperekezana pa siteji ya basi.
“Chomwe chinatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke nyanga ndi chakuti awiriwo sanagwirizane kuti maiyo adzabwelera liti koma patangopita tsiku limodzi iye anatulukira pa nyumbapo ndi khonyo la nandolo lija koma mdima utayamba ndipo atatula thumbalo anangoti gwilimindi ku chipinda komwe anapeza awiriwo akupanga zawozo pa bedi.
“Mosakhalitsa chindeu cha ndiwe yani chinabuka ndipo mkazi wakubayo akuti anavulidwa zovala zake zonse pamene mamunayo analiyatsa liwiro kuthawa koma mimba ili pamtunda,” iwo anafotokozera Maravi Express motere.
Nayenso mamuna wa mkazi wakubayo atamva izi akuti anatayira tiakatundu ta mkaziyo panja ndipo wanenetsa kuti ali mkati mofufuza mkazi wina woti akwatire pamene mkulu wampingoyo akuti sakudziwika komwe wathawira.