Afafanthidwa Modetsa Nkhawa Kamba Kochita za Dama ndi Mkazi wa Mwini

Wolemba: Richard Chinansi

Mamuna wina wa chimasomaso kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo akuti masiku apitawa anafafanthidwa modetsa nkhawa pamene anamupezelera akuchita za dama ndi mkazi wa mwini.

Malinga ndi kunena kwa bambo Gama omwe amachita geni ya Kabichi pamsika wa Bvumbwe, nkhaniyi yati mwini mkaziyo wakhala akukayikira za mayendedwe a mkazi wake maka-maka akapita kukachita geni yake ya Nkhuku pamsika omwewo wa Bvumbwe.

Anthu enanso akufuna kwabwino akuti akhala akutsina khutu mamunayo kuti mkazi wake akuyenda mwa mseli ndi njonda ina yomwe imagwira ntchito pa kampani ina ya zomangamanga yomwe ikumanga maofesi angapo kumeneko.
Koma akuti mamunayo akafunsa mkaziyo za mphekeserazo iye amakaniratu kwantu wa galu kuti sangachite zimenezo kamba koti ali ba banja lolemekezeka lomwe liri ndi ana atatu.

Ndiye paja akulu amati ukatambatamba adziyamba kaye wayang’ana kunyanja kamba koti kunja kungakuchere, awiriwo akuti tsikulo anapangana zoti akakumane pa nyumba ina yogona alendo nthawi ya nkhumaliro osadziwa kuti mwini mkaziyo anaganiza zokatchaya bawo pa malo ena oyandikana ndi nyumbayo.

Mamuna wachimasomasoyo akuti anadutsa pa bawopo ulendo wa ku nyumbayo osadziwa kuti mwini mkaziyo ankgangoyang’ana ndipo kenaka mamunayo anazemba nkukabisala kuseli kwa mpanda wa nyumbayo. Mosakhalitsa mkazi uja nayenso akuti anatulukila nkukalowa mu nyumbayo osadziwa kuti mamuna wake anali pambuyo kumulonda.
Apa mamunayo akuti sanaimve koma kugogoda ndi kuthyola chitseko cha chipinda chomwe anapeza awiriwo ali mbulanda akupanga zaozo.
Chindeu cha dzaoneni akuti chinabuka ndipo mkazi uja atawona kuti patelera anangotenga chitenje nkuliyatsa liwiro kuthawa koma zovala zake zones kuphatikizapo kabudula wa mkati zili mchipinda momwemo.
Khamu la anthu akuti linasefukila ku nyumbayo izi zitangomveka ndipo anthu ena ogwira ntchito pa nyumbayo akuti ndi omwe anapulumutsa bamboo wachimasomasoyo koma magazi ali chuchuchu mphuno ndi mkamwa ndipo nkhope akuti inali yotupa ngati wagundidwa ndi sitima.

Kenaka mwini mkazi uja akuti analiyatsansi liwiro kuthamangira kunyumba kutinso akakunthe mkazi wakeyo koma akuti sanamupeze koma mosakhalitsa anasonkhanitsa zovala zones za mkaziyo nkuzibutsa moto. Padakali pano mkaziyo akuti zakudziwika komwe ali koma mamunayo akuti wamenyanitsa nkwangwa pa mwala kuti banjalo laumapo.

Afafanthidwa modetsa nkhawa Atamupeza