Mbava ipezeka ili Mbulanda pa Denga

Wolemba: Richard Chinansi
Zina ukamva kamba anga mwala anthuni. Munthu wina yemwe akumuganizila kuti ankafuna kuthyola ndi kuba pa nyumba ya mkulu wina kwa Gayesi mumzinda wa Blantyre akuti anapezeka ali pa denga la nyumbayo koma ali chinochino.
Nkhaniyi yati mwini nyumbayo anadabwa pamene chitseko chake chinkamveka ngati pali munthu wina yemwe amalimbana nacho kuti athyole.
Izi zili choncho mwini nyumbayo akuti anayamba kukuwa pofuna kuti anthu oyandikana nawo adzuke ndi kumuthandiza pa zomwe zimachitikazo.
Atamva mkuwowo mbavayo akuti inathawira kuseli kwa nyumbayo yomwe ili mu mpanda wa njerwa ndipo itazindikira kuti khwimbi la anthu linayamba kufika inavula zovala zake nkukabisala pa denga la nyumbayo ndicholinga chofuna kupusitsa anthuwo kuti yathawa.
Koma paja akuluakulu amati tsiku la 40 likakwana mbavayo lake linayikwanila ndipo mwana wachichepere akuti ndiye anauza anthuwo kuti akuwona chinthu chodabwitsa pa denga la nyumbayo.
Anthuwo anaganiza zokwera pa dengalo ndipo mbavayo inadumpha koma inangofikila m’manja mwa anthuwo omwe sanachedwe koma kuyamba kayifafantha modetsa nkhawa.
Kenaka atayifunsa chomwe chimachitika iyo akuti inayankha kuti imatamba ndipo kuti yagwa mu ndege yomwe imadutsa pa denga la nyumbayo.
Anthuwo akuti anapitiliza kuumbuza mbavayo yomwe kenaka inaulula kuti inkafuna kuba mnyumbayo.
Khwimbi la anthuwo akuti linamenya mbavayo mpakana kuyikomola komanso nkhope inatupa kwambiri, maso kukwililika ngati yagundidwa ndi sitima.
Padakali pano sidzikudziwika ngati mbavayo yomwe anakayiponyera pa dambo lina kumeneko ili ndi moyo kapena ayi.