Mayi Waulemu Wake Amupezelera Akuchita Za Dama ndi Mnyamata Waganyu

Mayi wina ku Makhetha mumzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre akuti masiku apitawa anawona ngati kutulo pamene anamupezelera akuchita za dama ndi mnyamata wina yemwe anamulemba ganyu yokolora chimanga ku munda .
Izitu akuti zinachitika dzuwa litangopendeka pamene anthu masiku ano ali kalikiliki kukolora mbeu zawo.
Malinga ndi kunena kwa a Anthony Chisasa omwe ayandikana minda ndi wa banja la mayi wachimasomasoyo, iwo anati mamuna wake yemwe amakhala mdziko la South Africa wakhala akutumiza ndalama kwa mkazi wakeyo kuti apeze anthu ogwira ntchito ku mundawo ndipo zonse zakhala zikuyenda bwino mpakana nthawi ino yokolora. Mamunayo akuti anatumizanso ndalama zoti mkazi wakeyo apeze anthu angapo aganyu kuti amuthandize kukolora chimanga.
Maiyo akuti anapeza anyamata angapo oti agwire ntchitoyo ndipo tsiku litakwana ntchito inayambika kwinaku ena akututa chimanga kukasiya kunyumba.
Koma akuti chomwe chimadabwitsa aganyu enawo nchoti maiyo samakhala ndi chidwi chowona m’mene ntchitoyo imayendera koma kwake kunali kucheza ndi m’modzi mwa anyamata aganyuwo kwinaku akudekhelana maso.
Kenaka aganyu ena aja atamaliza zonse anawapatsa zawo ndipo anauyamba ulendo wa m’makwawo nkusiya mai uja ndi mnyamata uja pansi pa mtengo akukambirana.
Koma chomwe chinatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga ndi chakuti m’modzi mwa a ganyu aja anayiwala patapata zake m’munda muja ndipo atazindikila anabwelera kuti akatenge koma atangofika m’mundamo anapeza mai uja ndi mnyamata uja ali buno akuchita za dama. Atangowona izi mnyamata wa ganyu uja anatola buluku lake nkuliyatsa liwiro la ntondo wodooka pamene maiyo anangoti kakasi ngati nkhuku ya chitopa.
Padakali pano mbiri ili buu m’mudzimo ndipo sidzikudziwika kuti mamuna wa maiyo akamva nkhaniyi zidzatha bwanji. Maiyo akuti akungobindikila mnyumba kamba ka manyazi.