Mbava Yokuba Maungu Iwona Mbwadza Atayiwumbuza Ngati Yagundidwa ndi Sitima

Pamene anthu ali kalikiliki m’madera ambiri mdziko muno kukolora chimanga komanso mbeu zina monga maungu ndi nkhaka, mkulu wina anachitenga ichi ngati chinthu cha mwayi kuti nayenso akolore pamene sanalime.
Maravi Express yamvetsedwa kuti mkulu wina kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo wakhala akupita ku minda ya anthu osiyanasiyana kwa mfumu yaing’ono Chiwaya komwe wakhala akuba maungu nkumakawagulitsa mu msika wa Limbe kangapo konse.
Anthu ena ndiwo akuti anadabwa ndi mkuluyu popeza tsiku ndi tsiku amamuona pa malo ena okwelera basi ali ndi matumba angapo a maungu akukweza galimoto zolowera ku Limbe ndipo izi zinawadabwitsa.
Izitu m’mene zimachitika nkuti anthu angapo kumeneko atadandaula kale kuti samadziwa komwe maungu awo amapita popeza samapeza okhwima akafuna kuti akaphike kunyumba.
Kenaka anthu a m’mudzimo anatsinana khutu zoyamba kutsatira mayendedwe a mkuluyo ndipo paja akulu amati ukatambatamba udziyamba kaye wayan’gana kunyanja kamba koti kungakuchere ndipo iye kunamucheradi pamene anakumana nazo.
Monga mwa chizolowezi mkuluyo anafika pa siteji ya basi ndi thumba la maungu kenaka nkubweleranso m’munda wina kuti akanyamule lina. Atangolisenza ena mwa eni minda anamuyimitsa nkumufunsa kuti kodi munda wake ndi uti womwe wathyolamo maunguwo ndipo iye amangoti ichi wanena ichi wanena kenaka kakasi pakamwa.
Anamalirawo akuti anayamba kumukon’gontha atamuthira zingwe ndipo kenaka anamulamula kuti asenze matumba a maunguwo ulendo wa ku Polisi ya Bvumbwe.
Koma munjira nawonso achikumbe ena omwe akhala akubeledwa analowelera mu khamu la anthuwo nkumapupatsa matheche ndi mapama mokuti amatuluka magazi mphuno ndi mkamwa komanso nkhope yake inatupilatu ngati maungu amabawo.