Chikopa cha Galu ndi mutu zipezeka M’bali mwa Mtsinje wa Limbe

Koma maidya idyawa nthawi zina makamaka anthu okhuta mowa amatha kudya zosadya ndithu. Masiku apitawa akuti anthu ena omwe amalima madimba awo m’bali mwa mtsinje wa Limbe anapeza Chikopa ndi mutu wagalu pathengo lina loyandikana ndi msika waukulu wa Limbe.
Anthu amenewa akuti anayitanizana ndipo nawonso mavenda anakhamukila kukawona zinthu zimenezi.
Malinga ndi kunena kwa a Pitala Gama, anthuwo akuti galuyo akukhala ngati anagundidwa ndi galimoto ndipo palibe chikayikitso kuti anachita kusendedwa ndi munthu wina wankhanza yemwe nkutheka kuti amagulitsa baya-baya m’mashabini ozungulira msika wa Limbe.
“Nkutheka kuti angathe kusanganiza nyama ya galuyo ndi ya m’buzi ndipo anthu woledzera mowa sangathe kuzindikira chilichonse kamba koti kwawo kumakhala kukhwasula kuti achotse dalazi basi,” iwo anafotokoza motere.
Iwo anawonjeza kuti nthawi zina anthunso amatha kudyetsedwa kanyenya wa nkhuku zokufa zokha zomwe amazigula pa mtengo watsika kwambiri ndipo akakazinga kanyenya anthu amagula osadziwa kuti nkukhukuzo zinafa zokha.
Iwo analongosola motere, “Takhala tikuonanso nkhuku zina zomwe zimakhala kuti zaonongeka m’magolosale osiyana siyana zomwe zimayenera kukatayidwa ku ntaya zikugulitsidwa kwa anthu a geni ya kanyenya.”
Nkhani ngati iyi siyachilendo kamba koti zikuchitika m’madera ambiri ngakhale kuti a zaumoyo akhala akulimbikitsa anthu kuti sibwino kumadya nyama zokufa zokha komanso zoyenera kukatayidwa ku ntaya.