Mnyamata Adabwitsa abale ake atapezeka akukodzera m’beseni la Madzi

Zinthu zina abale kamba anga mwala anthuni. Banja lina ku Ndirande mumzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre lidawona ngati malodza pamene mwana wawo wa mamuna anamupezelera akukodzera m’beseni ya madzi yomwe anaiyika pakhonde pofuna kupeza madzi a mvula.
Izitu zinachitika ku dera lomwe limatchuka kuti Zambia mtaunishipi imeneyi ya Ndirande masiku apitawa.
Malinga ndi kunena kwa mkulu wina yemwe anangodzitchula dzina kuti Banda, mnyamatayo patsikulo anakhuta mowa wina wofanana ndi madzi ndipo mvula itayamba anapita kunyumba nkukagona.
Kenaka mikozo itamugwira anayenda ali dzandidzandi nkukayima panja nkuyamba kukozera mbeseni ya madzi a mvula aja.
Mayi wa mnyamatayo akuti atatuluka mkitchini momwe amaphika chakudya anapeza mnyamatayo akuyimilira mbeseniyo ndipo sanakhulupilire izi zikuchitika kenaka anathamangira pa mulu wa nkhuni nkutenga mtengo nkuyamba kuumbuza mnyamatayo yemwe analira chokweza.
Mosataya nthawi bambo wa mwanayo atamva izi nayenso sanaugwire mtima koma kuphaphalitsa makofi mwanayo yemwe mowa utamukungunuka anathawa.
Padakali pano mnyamatayo akuti akukhala kwa mkulu wake kwa Chemusa kamba koti anthu ku Ndirande mbiri ili buu pomanena kuti zomwe anachitazo zikusonyeza kuti ndi nthakati.