Ayimitsa Anthu Mitu Atapezeka Akujambulitsa Zithunzi Ali Mbulanda

Anthu ena omwe amakhala ku Chitawira mumzinda wa Blantyre masiku apitawa akuti anayima mitu pamene msungwana wina yemwe akumukhulupilira kuti ndi woyendayenda anali pa chi ntchito chotoletsa zithunzi kwa mkulu wina mu malo ochitira macheza aja amatchuka kuti Njamba Park dzuwa liri pa liwombo.
Malinga ndi kunena kwa bambo Emmanuel Banda omwe anawona izi zikuchitika maso ndi maso, iwo anauza Maravi Express kuti msungwanayo anafika pa malowo ndi chikwama chake nkukhala pansi pa mtengo kuyembekezera mkulu wotola zithunziyo.
Ndipo atangofika akuti awiriwo analowa pa kathengo kena komwe msungwanayo anayamba kuvula zovala zake chimodzi-chimodzi mpakana nkusala ndi kabudula wa mkati yekha.
Kenaka mkuluyo atayamba kutola zithunzi za msungwanayo, anthu ena anayitanizana kuti adzaone malodzawo koma akuti ngakhale kuti anthuwo amanka achulukilachulukila kwinaku akuzuma, msungwanayo izi sidzinamukhuze popeza amati akatoletsa zingapo zithunzi amapita kukasintha zovala makamaka zija amakonda kuvala amayi ku Nyanja mpaka anamaliza ndithu.
Amayi ena achikulire omwe anali pa malowo akuti ananenetsa kuti sangalole ana awo kuchita malodzawo kamba koti izi zimasonyeza kusowa chikhalidwe cha mtundu wa chi Malawi.
Anthuwo akuti anakuwiza msungwanayo pamene amatuluka pathengopo mpaka kumukakamiza kuti avale chitenje ngati amafuna kuti ayende bwino ulendo wa kwawo mwa mtendere.
Mkulu wotola zithunziyo akuti anazemba anthuwo pamene anadutsira njira ina yokatulukira kumseu.
Malipoti akuti asungwana ambiri makamaka woyendayenda akhala akuchita izi mu Njamba Park kwa nthawi yaitali ndithu.