Akulu a mpingo Agawana Ndalama za Mpingo Nkukagulira Zofuna Kumtima Kwawo

Zina ukamva anthuni kamba anga mwala akulu anatero. Anthu kwa Gwaza m’boma la Balaka akuti masiku apitawa anayima mitu pamene zinamveka kuti akuluakulu a mpingo wina anagawana ndalama zomwe bungwe lina linapereka pa mpingowo nkukagulira zofuna zawo.
Malinga ndi kunena kwa mayi Nadimba omwe amakhala pafupi ndi tchalichilo, akhristu kumeneko akhala akuchitira mapemphero awo mkachisakasa kwa zaka zingapo ndipo anagwilizana zoti amange kachisi watsopano. Pa ichi iwo anagwilizana zolembera kalata zingapo ku mabungwe a kunja omwe amathandiza mipingo munjira zosiyana siyana.
Mwamwayi wawo, bungwe limodzi lidavomera kuti liwathandiza zaka ziwiri zapitazo koma ndondomeko yake inali yoti awumbe njerwa pawokha komanso kututa mchenga ndi miyala chithandizocho asanachitumize.
Zitamveka izi akuti mochilimika akhristuwo pamodzi ndi anthu ena akufuna kwabwino anagwira ntchito mochilimika ndipo pamene chaka chatha chimafika mu Sepitembala nkuti zonse zitatheka ndipo nayonso uvuni inali itawotchedwa.
Otola zithunzi anagwira ntchito yawo ndipo pambuyo pake akuluakulu pa mpingowo anatumiza zithunzizo pamodzi ndi kalata kwa bungwelo lomwe liri ku limodzi mwa maiko aku ulaya kuti mwina angawaganizile pa dandaulo lawo kunkhani ya malata ndi simenti.
Mosakhalitsa akuti bungwelo linatumiza ndalama ku thumba la mpingowo zomwe kuchuluka kwake sidzinadziwike ndipo akuluakuluwo anangolengeza kwa akhristuwo kuti ndalama zafika.
Koma akhristuwo anadabwa kamba koti miyezi imapita koma osamuona ndi m’modzi yemwe bilidala pa mpingowo. Kenaka akhristuwo anayamba kudabwa kamba koti amati akalowa mnyumba ya mkulu wa mpingo uyu amapeza mwasinthiratu, akapita kwa mlembi amapeza zonse za pa balaza ndi zatsopano, akati apite kwa mkulu wa amayi iyayi amapeza watsegula wokala chinthu chomwe chinawapangitsa kudabwa kuti ndalama zogulira katunduyo anazitenga kuti.
Atawakhamitsa malovu akuti m’busa wa pa tchalichilo pamodzi ndi akuluakulu a mpingowo ananena kuti anagwiritsa ntchito ndalamazo ndipo anali pa chi ntchito chofunafuna kuti azibweze.
Padakali pano akuti mpungwepungwe ndiwo wadya mlemeko pa mpingowo pamene ena mwa akulu ampingo achinyengowo asamuka mnyumba zomwe amakhala ndipo sakudziwika komwe alowera.