Mwana Aseweretsa Njoka koma Osalumidwa

Anthu ena kwa Likoswe m’boma la Chiladzulu akuti anazizwa kamba koti mwana anapezeka akuseweretsa njoka koma sinamulume, Maravi Express yamvetsedwa motere.
Malinga ndi kunena kwa mkulu wina yemwe amachita geni yogulitsa nkhuku pa msika wina kumeneko, banjalo patsikulo linapita kumunda kukapalira Chimanga pamodzi ndi anthu ena omwe anawalemba ganyu.
Atafika kumundako maiyo akuti anakhazika mwana wake wachichepere pansi pa mtengo wa Mango osadziwa kuti chapafupi panali njokayo.
Kenaka kupalira kuli mkati mai uja anaganiza zokazonda mwanayo pansi pa mtengo paja.
Koma atangofika anachita nthumazi kuona mwana uja akugwira njokayo ndipo anathamanga nkukafotokozera mamuna wake ndi anthu ena aja za chilombocho.
Koma pamene anthuwo anafika ndi miyaka komanso ndodo zawo pa malopo kuti aphe njokayo akuti anapeza palibe komanso mwanayo sanalumidwe pali ponse. Anthuwo anayesetsa kufufuza njokayo kuzungulira malowo koma zadayipeze.
Anthu kumeneko akuganiza kuti njokayo inali ya matsenga kuchokera kwa mkulu wina yemwe wakhala akulimbirana ndi banjalo kunkhani ya malire a mundawo.