Afafanthidwa Modetsa Nkhawa Atapezeka mu Nyumba Yogona Alendo ndi Mamuna wa Mwini

Koma asungwana enawa sadzamva ku nkhani yogona ndi amuna ayeni. Msungwana wina woyendayenda ku Bangwe mumzinda wa Blantyre akuti masiku a chisangalalo cha khisimasi ndi chaka chatsopano anawona zakuda m’malo mokonwelera nyengoyi.
Nkhaniyi yati pamene anthu amakondwera kutsanzikana ndi chaka cha 2016 m’madera ambiri mdziko muno maka kumbali yoti ambuye mulungu watisunga ndi moyo chaka chimenechi, nawonso asungwana ambiri amachiwona ichi ngati chinthu cha mtengo wa patali kuti agonane ndi amuna a eni m’malo ogona alendo osiyana siyana kuti aphe makwacha.
Ndiye akuti usiku wa pa Disembala 31, msungwanayo anatchena nkupita ku malo ena omwera mowa komwe amuna ambiri kuphatikizapo njonda ina anamugulira mowa mpakana kuledzera ngati kulibe mawa.
Kenaka akuti nthawi itangokwana 12:00 makombola akuphulika kutsonyeza kuti chaka cha 2017 chafika awiriwo anaganiza zopita kukagona ku malo ena omwe ali pafupi ndi balayo.
Anthu ena akuti usiku omwewo anatsina khutu mkazi wa njondayo wa kunyumba kuti anawona awiriwo akupita ku nyumbayo koma iye akuti sanatutumuke ndi izi polingalira kuti nazonso mbaza zimakonda kuthyola nyumba mu nyengo imeneyi.
Koma kunja kutangoti mbuu akuti maiyo anapita pa chipata cha nyumba yogona alendoyo pamodzi ndi anzake angapo kukhala ngati akuwonelera m’ene anthu amatsilizira chikondwelero choti alowa chaka cha tsopanochi.
Kenaka akuti awiriwo atangotuluka pa chipata cha nyumbayo amayiwo anangoti naye msungwana woyendayenda uja gwiro nkuyamba kumufafantha mosapsyatira mpakana kumuvula zovala zake zonse kwinaku magazi ali chuchuchu mkamwa ndi mphuno.
M’mene izi zimachitika nkuti mamuna wa mkazi uja atathawa nkukabisala mu nyumba ina kumeneko.
Kenaka akuti anthu ena anayamba kulesetsa msungwanayo ndipo pamenepa anapeza mpata nkuyamba kuthawa kudutsa pa msika wa mvula ndi kabudula wa mkati yekha koma kwinaku khwimbi la amayi ndi ana likuyimba nyimba zomutonza amvekere ‘huleyo, huleyo, huleyo.
Kenaka akuti iye anadya makona angapo kenaka osawonekanso ndipo mwini mamuna uja pamodzi ndi anzake aja anauyala wobwelera kunyumba. Padakali pano mamuna wa chimasomasoyo akuti sakudziwika komwe ali.