Wamisala Adabwitsa Anthu Atathawitsa njinga Kenaka Nkubwelera Nayo Patapita Maola Angapo

Athu ochita malonda pa msika wina mb’oma lotchuka kunkhani yolima mbeu ya tiyi ku Thyolo akuti anafa ndi phwete pamene wamisala wina anathawitsa njinga ya mkulu wina yemwe panthawiyo amataya madzi .
Nkhaniyi yati mkuluyo yemwe amagwira ntchito pa imodzi mwa mafakitale kumeneko anayimitsa njinga yake nkulowa mu tiyimo kuti ataye madzi ndipo asanatero anauza makosana ena omwe amasewera bawo pakhonde la wokala ina kuti amuyang’anire.
Koma akuti atangoyimika njingayo, wamisala wina yemwe amazungulira m’misika kumeneko anavumbuluka ngati kamvuluvulu nkukwera njingayo yomwe anatchova mwa mtima bii moti anthu omwea amuthamangila ndi njinga zawo sanamupeze mpakana osamuwonanso.
Apa mwini njingayo akuti anathedwa nzeru ndipo anangokhala chiyimire pa wokalayo manja ali mkhosi kanga koti ankawona ngati ndi malodza. Iziti akuti zimachitika chakum’mawa anthu ochita malonda pa msikawo ali pikitipikiti.
Amene auza Maravi Express nkhaniyi bambo Delison Mahere anati patapita maola pafupifupi asanu ndi awiri wamisalayo anatulukira ndi njingayo thukuta liri kamukamu nkudzaiyimitsa pomwe anayitenga paja.
Apa anthu omwe anali pa malopo akuti anachita chiphwete ngati kulibe mawa uku nkuti mwini njinga uja atanyamuka wa kunyumba kwinaku akugwedeza mutu. Wamisalayo akuti ankangoseka pamene izi zimachitika ndipo mosakhalitsa anachoka pa malowo.