Agamulidwa Zaka Khumi ndi Ziwiri Ku Jere Kamba Kogwililira Ana Okhala Ake Omwe

Koma anthu ena ayi ndithu. Khothi la majisitireti loyamba la m’boma la Kasungu posachedwapa lidalamula njonda ina ya zaka 29 kuti ikakhale kundende kwa zaka khumi ndi ziwiri atapezeka olakwa pa mlandu ogwililira ana ake awiri.
Anawo akuti ndi a zaka zisanu ndi ziwiri (7) komanso zisanu ndi zinayi (9).
Mkuluyo yemwe sanatchulidwe dzina pofuna chitetezo anamunjata pa 23 Novembala kamba ka mchitidwewo womwe akuti wakhala akuchita kwa zaka ziwiri tsopano.
Izi akuti zinaululika kamba koti mwana wa zaka 7 anauza ena achibale zomwe mkuluyo amachita. Apa achibalewo anayitengela nkhaniyi ku polisi komwe inapitilira mpakana ku khoti la malamulo komwe iye anavomereza ndipo anapempha khothi kuti limuchepetsere chilango kamba koti aka kanali koyamba kulakwa.
Koma oyimira apolisi pa mlanduwo a Jennings Mkandawire anapempha khothi kuti lipatse wolakwayo chilango chokhwima kuti ena atengelepo phunziro.
Ogamula mlandu a Damiano Banda anagwirizana ndi a Mkandawire kuti mkuluyo amafunikadi chilango chokhwima chomwe anamupatsa kuti akakhale ku jere zaka khumi ndi ziwiri.
Mkulu wa mchitidwe woyipa mtima ngati motoyo amachikora pa mudzi wa Chiswe mdera la mfumu yaikulu Chikumbe m’boma la Mulanje.