Agwetsa Kachisi Kamba Kosamvana Maganizo Kunkhani Ya za Chuma

Dzikoli kaya likulowera kuti anthuni? Akhristu pa mpingo wina kwa Ntopwa mtaunishipi ya Bangwe munzinga wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre masiku apitawa akuti anagwetsa Kachisi kamba kosamvana maganizo ndi m’mene akuluakulu akhala akuyendetsela ndondomeko ya za chuma.
Malinga ndi kunena kwa a James Milanzi omwe amakhala kwa Ntopwako pafupi ndi tchalitchilo, akhristuwo akuti akhala akudabwa ndi m’mene chuma chakhala chikuyendela pa mpingowo maka popeza ntchito yomanga kachisiyo inali ikupitilirabe.
“Akhristuwo akuti akhala akupereka moolowa manja kwa zaka zapitazi koma chomwe chimawadabwitsa nchoti zipangizo zomangila kachisiyo zomwe zakhala zikugulidwa zinali zochepa kwambiri kuyelekeza ndi maperekedwe awo.
“Akhristuwo akuti kangapo konse akhala akufunsa akuluakulu pa mpingowo kuti awafotokozere tsatanetsatane wa m’mene chuma chimayendera kunkhani ya mamangidwe koma akuluakuluwo amangoti ichi akamba ichi akamba,” a Milanzi anauza Maravi Express motere.
Kenaka akhristuwo akuti anayitanizana kumbali nkukambilana zokhamisa malovu akuluakuluwo kuti afotokoze ndondomeko ya zachumayo mwa mvemvemve ndipo anakonza tsiku lapadera kuti mbali ziwilizo zikumane.
Atakumana akuti palibe chanzeru chomwe akulu ampingowo adakamba pa nkhaniyo ndipo mosataya nthawi akhristu okwiyawo anayamba kugwetsa mawindo, zitseko komanso zikupa za tchalichilo kwinaku akulu ampingowo akuliyatsa liwiro la ntondo wodooka kuthawa.
Khwimbi la anthu akuti linasonkhana pa malowo ndipo nawonso a tsinzinantole anatenga ichi ngati chinthu cha mwayi pamene ananyamula wina mwa katundu pa malowo kuti akagulitse.
Padakali pano tchalichilo akuti langotsala ngati bwinja ndipo mapemphero sakuchitikanso.