Avulazidwa Molapitsa Kamba Kopezeka Kuchipinda Mnyumba ya Mwini

Mkulu wina ku Bangwe mumzinda wa Blantyre masiku apitawa anaphopholedwa molapitsa kamba koti anapezeka kuchipinda cha nyumba ina yoyandikana nayo ali gonee pa kama.
Malinga ndi omwe atofotokozera Maravi Express nkhaniyi, mkuluyo akuti wakhala ali paubwenzi wamseli ndi mkazi wa mzake wa nyumba yoyandikana nayo ndipo awiriwo akhala akumakumana mnyumbamo mwini mkaziyo akapita kuntchito ya ugadi mtauni ya Limbe.
Anthu akuti akhala akunon’goneza gadiyo za nkhaniyi koma iye samakhulupilira kuti izi zimachitikadi ati kamba koti akhala kupapila limodzi mowa m’mabala ndi mzakeyo.
Koma paja amati likakwana lafote, zinthu akuti zinafika pa indeinde pakati pa awiriwo kamba koti mamuna wakubayo sali pa banja ndiye amangolowa mnyumba mwa gadiyo m’mene akufunila akachoka.
Nkhaniyi yati patsikulo gadiyo anatsanzika mkazi wake kuti wayamba wapita kumudzi kukatenga chimanga ndipo apa mpamene anawona ngati mwayi kuti akhale malo amodzi ndi chibwenzicho.
Atadekhelana maso awiriwo analowa mnyumba mpakana kuchipinda. Maiyo akuti anauza mamuna wakubayo kuti akulowa kaye m’bafa kuti akasambe.
Koma akusamba anadabwa kumva chiphokoso mnyumbamo ndipo atasunzumila anawona mamuna wake uja akuphophola mzake wakubayo ndipo apa mai wachimasomasoyo anadziwa kuti zake zada ndipo kenaka anangovala zovala zake nkuyenda zamadulira.
Anthu akufuna kwabwino kuphatikizapo mwini nyumbazo akuti ndi omwe anapulumutsa mamuna wakubayo koma ali magazi okhaokha mkamwa ndi mphuno komanso nkhope yonse itatupa ngati wagundidwa ndi sitima. Padakali pano akuti mamuna wakubayo watenga katundu wake ndipo sakudziwika komwe wapita pamene mwini mkaziyo ati wanenetsa kuti banja laumapo.