Mayi Wina Aphopholedwa ndi kuvulidwa Kamba kochitira Nsanje Mamuna wa Mwini

Mayi wina ku Bangwe mumzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre masiku apitawa anawona ngati ku tulo pamene anaphopholedwa molapitsa ati kamba kochita nsanje ndi mwini mamuna.
Nkhaniyi ikuti maiyo wakhala akuyenda ndi mamuna wa mwini kwa zaka zingapo koma wakhala akupanga izi ndi izi kuti alande mwini banjalo yemwe amangwira ntchito ngati dotolo pa chipatala china kumeneko.
Kenaka amayi awiriwo akuti atakumana pa malo okwelera basi kunali kuphopholana osati masewera koma mwini banjalo mothandizana ndi anzake omwe analowelera ndeuyo akuti anafafantha mai wakubayo mpakana kumuvula mbulanda.
Anthu achifundo akuti ndi omwe analesetsa mai wakubayo ndi kumuthawitsa ndipo padakali pano akuti wathawa akukhala kwa makolo ake ku Mpemba.
Mamuna wa dotoloyo akuti akuyenda zolizoli ngati nkhuku ya chitopa kamba ka nkhaniyi moti nthawi zambiri akumafika kunyumba kwake kunja kukada.
Nkhani ngati izi zakhala zikuchitika m’madera ambiri mziko muno.