Azikhweza Pambuyo podziwa kuti mkazi wake ali ndi Mamuna wina

Mkulu wina ku Ndirande Makata posachedwapa akuti anazimangilira kamba koti anazindikila kuti mkazi wake anapalana ubwenzi wamseli ndi njonda ina yomwe imayitanira minibasi pa msika waukulu kumeneko.
Malipoti omwe afikila Maravi Express ati maiyo pa tsikulo sanagone kunyumba kwake koma anakagona kwa mamuna wakubayo.
Kutacha maiyo anapita kunyumbako ndipo mamunayo atamufunsa komwe anali iye ananenetsa kuti anagona kwa abale ake kamba koti kunja kunamudela.
Apa akuti awiriwo sanamvane Chichewa ndipo kenaka maiyo akuti anauyamba ulendo wopitanso kukagona kwa njonda yoitanira minibasiyo.
Mamunayo atazindikila izi akuti anangoganiza zozikhweza kuti ayiwale mavutowo.
Mkulu yemwe wafotokozera Maravi Express za nkhaniyi anapitilira nkunena kuti anthu kumeneko atazindikila izi anapanga dongosolo lokakumba manda ku Namalimwe.
“Achinyamata omwe amakumba dzenje la mandawo ambiri analedzera ndipo bokosi la mtembowo pamene limafika kumandako nkuti atangokumba kulekela m’mawondo ponena kuti malemuyo anachita chibwana cha mchombo lende podzimangilira kamba ka mkazi.
“Kenaka anthu ena akufuna kwabwino ndiwo anapitiliza kukumba mandawo mpakana maliloro anayikidwa,” iwo anafotokozera Maravi Express motere.
Padakali pano mkaziyo akuti wathawa ndipo sakudziwika komwe ali kamba ka nkhaniyi.
Tili ku Ndirande komweko mnyamata wina akuti waotchedwa ku Makata kamba koti wakhala akubela anthu makamaka amayi omwe amagwira ntchito zosiyana siyana mumzinda wa Blantyre.