Akhapa Bambo wa Mwana Wofuna Kugwililidwa Poyesa kuti Ndiye Amafuna Kugwilira

Zina ukamva kamba anga mwala anthuni. Anthu okhala mtaunishipi ya Zingwangwa mumzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre anazidwa komanso kuchita nthumazi kamba ka nkhani yomwe yafikila zikuchitika pozachedwapa.
Malipoti ati mkulu wina yemwe amachita bizinezi yowonetsa kanema mumsikawo masiku apitawa anayitanila mwana wosakwana zaka khumi mu nyumba yomwe amawonetsela kanemayo momwe anayamba kumugwilagwila pofuna kumugwililira.
Koma amayi ena ogulitsa nkhuni pafupi ndi nyumbayo anadabwa poona kuti chitseko cha nyumbayo chinakhomedwa.
Amayiwo anafotokozela anyamata ena omwenso amachita geni pa malowo omwe anathyola chitseko cha nyumbayo ndipo anapeza buluku la mkuluyo liri mawondo koma ali jijili-jijili ndi mwanayo. Apa anyamatawo anamugwila nkumumanga.
Kenaka nkhaniyi anayitengela kwa wapampando wa mumsikawo yemwe analamula kuti mkuluyo pamodzi ndi mwanayo apite nawo ku polisi ya Chilobwe.
Anthuwo akuti ali paulendo wa ku polisiko bambo wa mwanayo yemwe amagwila ntchito yokonza mu nyumba ina anamvetsedwa izi ndipo analiyatsa liwilo kuthamangila pa nyumba yowonetsela kanemayo.
Atangofika akuti anapeza khwimbi la anthu liri pa malowo kukambirana za malodzawo ndipo mosakhalitsa mnyamata wina akuti anakhapa bambo wa mwanayo ndi chikwanje pomuganizila kuti ndi mkulu yemwe amafuna kugwilira uja.
Koma zitadziwika kuti iye anali bambo wa mwana uja anthuwo akuti anagwilanso mnyamata yemwe anatema mkuluyo ulendo nayenso ku polisi ya Chilobwe.
Pamene zikuchitika imatsindikiza nkhaniyi nkuti zisakudziwika kuti zonse zinatha bwani ku Polisi ya Chilobweko.