Akomoledwa Atapezeleledwa Akuchita za Dama ndi Mamuna wa Mwini

Msungwana wina woyendayenda ku Makhetha mumzinda wa Blantyre akuti masiku apitawa anaumbuzidwa mpakana kukomoka atamupezelera akuchita za dama ndi mamuna wa mwini.
Mayi Falawo omwe anaona izi maso ndi maso anafotokozera Maravi Express kuti msungwanayo wakhala akuchita mchitidwe omadekhela maso ndi kumagona ndi amuna ayeni kwa nthawi yaitali m’mabala osiyanasiyana kumeneko.
Ndiye paja akulu amati ukatambatamba udziyamba wayang’ana kunyanja chifukwa choti kungakuchere, tsiku lake lachiweluzo linafika pamene anakumana ndi zokhoma.
Nkhaniyi yati mkulu wachimasomasoyo anapita kukapapila mowa pa bala ina yoyandikana ndi kunyumba kwake ndipo atayamba kuledzera anayitana msungwanayo nkuyamba kupapila mowawo limodzi.
Kenaka awiriwo anagwirizana zoti akagone kunyumba kwa msungwanayo ndipo zonse zinali tayale chonsecho osadziwa kuti mwini mamunayo pamodzi ndi amayi ena anabisala malo ena nayamba kulondola awiriwo.
Atalowa myumba anayamba kupanga za dama koma asanakhome chitseko kamba ka kuledzela. Mwini mamunayo ndi anzake aja anagofikila gwilimindi kulowa mnyumbamo ndipo anapezelera awiriwo ali pa mphasa ndipo mosakhalitsa anayamba kuphaphalitsa ndi zibagera chonsecho ali chinochino.
Ataona kuti pachema mkuluyo akuti anangotenga buluku lake lomwe analivalira munjira uku ataliyatsa liwiro la ntondo wodooka.
Anthu ena achifundo ndi omwe anathandiza msungwanayo mpakana kutsitsimuka.
Padakali pano mkuluyo akuti sakudziwika komwe ali pamene msungwana woyendayendayo akuti wasamukila kwa Kachere.
Mwini mamunayo akuti wamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti banjalo laumapo.