Apalana Ubwenzi Wamseli ndi Mayi Komanso Mwana

Mkulu wina ku Nancholi mumzinda wa Blantyre akuti wakhala akuyenda ndi mayi wina kuphatikizanso wana wake wamkazi woyamba Maravi Express yamvetsedwa motere.
Malinga ndi kunena kwa bambo wina yemwenso amakhala ku Nancholi komweko wati mkuluyo yemwe ali ndi banja lake lokhazikika anapalana unbwenzi wamseli ndi mayi wina wochita bizinesi yemwenso ali pa banja.
Ubwenziwo akuti wakhala zaka zingapo kamba koti mamuna wa maiyo anapita mdziko la South Africa kukagwira ntchito zaka zingapo zapitazo.
Koma kenaka mkuluyo akuti anayamba kudekhera maso m ’modzi mwa ana a maiyo pamene anayamba kumufumbatitsa ndalama komanso samawonetsa chidwi kwa maiyo ngati m’mene zimakhalira pachiyambi.
Kenaka ubwenzi ndi msungwanayo unafika pa inde-inde ndipo anthu ena anatsina khutu maiyo za chomwe chinali kuchitika pakati pa mwanayo ndi mkulu wopanda khalidweyo.
Atamufunsa akuti mwanayo ananenetsa m’maso muli gwaa kuti sangasiyane ndi njondayo yomwe inapupangila lendi ku Zingwangwa.
Popsya mtima ndi izi maiyo akuti anapita kunyumba ya mwanayo komwe chindeu cha dzaoneni pakati pa kholo ndi msugwanayo chinabuka koma anthu ena oyandikila nyumbayo ndiwo analekanitsa awiriwo.
Padakali pano msungwanayo akuti sakuwoneka komwe akukhala koma mamuna wa maiyo akuti adakalibe ku South Africa ndipo pali chiopsezo choti akadzabwelera kuno kumudz banjalo lidzatekeseka kapena kutha kumene kamba koti paja akulu amati mbiri sigonera.