Akozedwa Atapapira Mowa pa Mwambo wa Chikwati

Zina ukamva amati kamba anga mwala anthuni. Mnyamata wina yemwe amapanga bizinesi ya zitsulo za njinga ku Chirimba mumzinda wa Blantyre akuyenda wera wera ngati nkhuku ya Chitopa kamba koti anakozedwa mu holo pa mwambo wa Chikwati cha mlongo wake sabata yatha.
Malinga ndi kunena kwa m’modzi mwa anthu omwe anawonelera mwambowo a Justin Kanje omwe amakhala ku Chilomoni, zinthu zonse pa tsikulo zinayamba bwino pamene ukwatiwo unadalitsidwa ku limodzi mwa matchalichi kumeneko.
Kenaka itatha nthawi ya chakudya chikwaticho chinafika mu holo momwe munafika anthu ochuluka ochokera mbalizonse kuchimuna ndi kuchikazi komanso anthu ena akufuna kwabwino.
Koma itafika nthawi ya perekani perekani, anthu anadabwa pamene mnyamatayo anatulukira koma ali zandi-zandi kulowera kutsogolo kuti akafupe.
Atafupa ndi kubwelera pa mpando anayamba kugona tulo mwambowo ukupitilira koma mosakhalitsa anthu anadabwa atawona mikozo ikuyendelera pa malo omwe anakhalawo.
Anthu omwe anali naye pafupi anayamba kusuntha kenaka akuwowoza mnyamatayo yemwe panthawiyo anali thapysa.
Achinyamata ena anakokera mnyamatayo panja koma atakwiya kwambiri . Mwambo wachikwaticho akuti unayenda bwino kupatulapo nkhani imeneyi.
Padakali pano mnyamatayo akuti wathawa pakhomo pa makolo ake ndipo akukhala pa nyumba ina ya lendi ndi mzake.