Mphunsitsi Wankulu Asambitsidwa Ndi Zibagera ku Bangwe

Mphunzitsi wankulu wa pa sukulu ina yapulaimale ku Bangwe masiku apitawa anasambitsidwa ndi zibagera zomwe zinavumbwa kuchokera kwa makolo omwe anakwiya kamba koti m’modzi mwa aphunzitsi anamenya ndi kukomola mwana wasukulu.
Malinga ndi malipoti omwe afikila Maravi Express, m’modzi mwa aphunzitsi kumeneko anamenya ndi kukomola mwana wachichepere, chinthu chomwe chinapangitsa makolo komanso anthu ena omwe amagulitsa katundu wosiyanasiyana kumeneko kulowa mumpanda wa sukuluyo momwe anafuna kumva bwino lomwe chomwe chinachitika.
Nawonso ophunzira sanaimve koma kutseka msewu kwinako akuyimba nyimbo zosonyeza kukwiya ndi nkhanza zomwe aphunzitsi ena akuti akhala akuchitila ophunzira makamaka kunkhani ya zikwapu.
Anthuwo akuti mphunzitsi wankuluyo atayamba kulongosola sanamvane naye ndipo mosakhalitsa anayamba kumuphaphalitsa ndi makofi.
Anthu ena achifundo akuti ndi omwe anapulumutsa mphunzitsiyo kwa anthuwo koma akuti makolo a mwanayo anenetsa kuti nkhaniyi saisiyira pomwepo.
Maravi Express inatsindikizanso nkhani ngati imeneyi masiku apitawa yomwe inachitika ku sukulu ya Makata mtaunishipi ya Ndirande komwe mphunzitsi wina anamenya ndi kukomolanso ophunzira wachichepere kamba koti amataya madzi pa mpanda.
Nkhani yaku ndirandeko idakafikisidwa ku polisi ndi makolo a mwana yemwe anakomoledwayo.