Chimbalangondo Chiwotchedwa ku Bangwe Kamba kakuba ma Babu

Koma zinazi munthu ukamva sungazimvetsetse kamba ka zinthu zomwe zachitika masiku apitawa ku Mbayani mtaunishipi ya Bangwemumzinda otchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre.
Bambo wina kumeneko wataya moyo wake atamupeza akuchotsa ma babu pa ina mwa nyumba zamumpanda kumeneko.
Malipoti omwe afikila Maravi Express akuti mkuluyo wakhala akuba zinthu zina ndi zina kuphatikizapo mbaula ndi mapoto.
Ndiye patsiku lake la 40 litakwana iye anaganiza zokwera mpanda nkuyamba kuchotsa ma babu a nyumbayo.
Koma alonda atamuona anayamba kumuthamangitsa ndipo kenaka atamugwira khwimbi la anamalira makamaka achinyamata linasonkhana ndikuyamba kumuumbuza modetsa nkhawa.
Izi zili nkati ena akuti anathamanga nkutenga matayala nkumuveka mkhosi kenaka petulo anathilidwa nkumubutsa moto.
Mbavayo akuti inalira mokweza koma anthuwo anali kuiyimba nyimbo namanena kuti anthu ena omwe amakhala ndi maganizo opotoka maka pobela anzawo katundu yemwe amukhetsera thukuta atengelepo phunziro.
Pamene Maravi Express imatsindikiza nkhaniyi nkuti anthu achitetezo kumeneko atauzidwa kuti adzadziwonere okha malodzawo.
Nkhani ngati izi zakhala zikuchitika m’madera ambiri mdziko muno koma apolisi akhala akulangiza anthu kuti asamatenge lamulo nkuliyika m’manja mwawo popeza mbava zimayeneleka kupita ku khoti komwe amakagamulidwa pa zolakwa zawo.