Amwalira ndi Mowa Wachilendo Kamba Kosadyera

Mkulu wina yemwe anali wa zaka zakubadwa makumi asanu ndi mphambu imodzi (60) akuti masiku apitawa anataya moyo wake kamba komwa mowa wina wofanana ndi madzi koma osadyera.
Malemuyo yemwe dzina lake ndi Kalata Mdukamwera akuti anali mbiyang’ambe kwambiri ndipo ankakhalira moyo wake wa tsiku ndi tsiku pogwira ganyu kapena kuti zija ena akuti magobo masiku ano.
Anafotokozera atolankhani nkhaniyi ndi m’modzi mwa abale a malemuyo a Yosofati Chilooko.
Patsikulo akuti malemuyo anauza abale ake kuti akupita ku mudzi wina woyandikana nawo kuti akafune ganyu pa umodzi wa minda ya mpunga kumeneko.
Koma akuti atatero sanabwelerenso kunyumba kwake ndipo anapezeka atafa ndi ana ena omwe amasaka ziwala pafupi ndi mudziwo ndipo malipoti atafika kumudzi anthu kumeneko anatumiza uthenga ku polisi.
Malinga ndi kunena kwa m’neneli wa apolisi ya Nkhotakota a Williams Kaponda, apolisi pamodzi ndi anthu ogwira ntchito za chipatala anafika pa malo omwe anagona malemuyo ndipo zinatsimikizika kuti mkuluyo anamwalira kamba koledzera kwambiri koma osadyera.
Bambo Mdukamwera amachokera pa mudzi wa Kanyangale mdera la mfumu yaikulu Mwadzama m’boma lomwelo la Nkhotakota.
Nkhani za imfa zokhudzana ndi kumwa mowa waukali koma osadyera zakhala zikuchitika m’madera ambiri a mdziko muno