Mphunzitsi Amenya ndi Kukomola Ophunzira

Anthu ena akhala akudandaula kunkhani ya nkhanza zomwe aphunzitsi ena akhala akuchitira ophunzira msukulu zina mdziko muno. Izitu zatsimikizika pamene mphunzitsi wina anamenya ndi kukomola ophunzira masiku apitawa.
Nkhaniyi inachitika pa sukulu ya pulayimale ya Makata mtaunishipi ya Ndirande mumzinda wa Blantyre.
Malinga ndi kunena kwa bambo Banda omwe anawona izi zikuchitika maso ndi maso, mphunzitsiyo yemwe amaphunzitsa mu kalasi 7 pasukulupo anawona ophunzira wa Kalasi 4 akukoza pa mpanda.
Kenaka mphunzitsiyo anazembera mwanayo ndi kumukuntha mbama yomwe anagwa nayo pansi mpakana kukomoka.
Aphunzitsi ena akuti ndiwo anathandiza mwanayo kenaka nkuyitanitsa makolo ake kuti amutengere ku Chipatala.
Koma akuti aphunzitsiwo anauza makolowo kuti akapereke kalata yomwe anayilemba mwa bodza la nkhukuniza kuti ophunzirayo anangogwa ndi kukomoka payekha.
Koma makolowo atamva mvemvemve za nkhaniyi kuchokera kwa anthu ena oyandikila pa sukulupo akuti anapita ku polisi ya Ndirande komwe anatulira a zamalamulowo nkhaniyi mwa tsatane tsatane.
Pamene Maravi Express imatsindikiza nkhaniyi nkuti apolisiwo atakoka mphunzitsiyo kuti afufuze bwino lomwe chomwe chinachitika kuti ophunzirayo afike mpakana pokomoka.
Nawonso ophunzira ena pa sukuluyo akuti anatsimikizira makolo a mwanayo kuti anawona mzawoyo atagwa mpakana kukomoka kamba komenyedwa ndi mphunzitsiyo.
Izi akuti zakwiyitsa kwambiri makolo a ana omwe akuphunzira pa sukuluyo omwe anenetsa kuti atsatira nkhaniyi mpakana chilungamo chake chiwonekere poyera.