Akhakhathana Ndi Zikwanje Kamba Kolimbirana Malire

Kunali chindeu cha ndiwe yani makamaka chokhakhathana ndi zikwanje pakati pa maanja awiri omwe amakhala pa mapuloti ena kwa Nkwate ku Machinjiri mumzinda wa Blantyre, Maravi Express yamvetsedwa motere.
Malinga ndi kunena kwa mayi wina yemwe anangodzitchula kuti ndi a Nansefu omwe amakhalanso pafupi ndi maanjawo, izi akuti zinayambika pamene chimbudzi cha banja lina kumeneko chinadzadza ndipo analemba aganyu omwe anayamba kukumba china m’malire ndi puloti inayo.
Koma poona izi mayi wa banja linalo anatchayira thenifolo mamuna wake nkumuuza kuti banja linalo limawalowelera malire awo ndiponso amakumbapo chimbudzi.
Mkuluyo akuti sanaupeze mtima koma kuthamangila kunyumba komwe anazazila aganyuwo nkuwauza kuti alekeletu kukumba chimbudzicho kamba koti anali malo awo.
Aganyuwo sanavute ndipo analeka kukumba chimbudzicho kamba koti mwini ntchitoyo pamodzi ndi mkazi wake nawonso anali atapita ku ntchito. Mosataya nthawi mkulu uja akuti anatenga fosholo nkuyamba kukwilira dzenje la chimbudzicho kwinaku akulalata kwambiri.
Atafika madzulo mkulu yemwe amakumbitsa chimbudzi uja atamva za nkhaniyi anapita kunyumba ya mzakeyo komwe pambuyo pokangana winayo anatenga chikwanje chomwe anavulaza nacho mzakeyo ndipo ana a ovulazidwayo nawonso anatenga zitsulo nkuyamba kuumbuza nazo mkulu okhapa mzake uja.
Anthuwo akuti anavulazana kwambiri kamba koti enanso achibale cha maanjawo analowelera chindeucho chomwe chinali cha chisawawa komanso chinavuta malesetsedwe ake. Malipoti akuti ovulazidwawo anathamangila nawo ku chipatala.
Padakali pano, maanja awiriwo akuti sakuwonana ndi diso labwino pamene akudikila kukawonekera kwa akuluakulu mdelaro omwe akuyenela kukaweruza za malire enieni a mapulotiwo.