Athamangitsa Mkazi Wake Kamba Komulalatira Ali Mchipatala

Mkulu wina ku Lirangwe akuti wathetsa banja lake kamba koti mkazi wake sanamulankhule bwino pamene anali mchipatala Maravi Express yamvetsedwa motere.
Malinga ndi kunena kwa mkulu wina yemwe amacheza ndi bamboyo, nkhaniyi yati mkuluyo anayamba kudwala m’mimba ndipo anagonekedwa pa Chipatala cha Mlambe masiku apitawa.
Koma akuti mkazi wakeyo amanyinyilika zokagoneka matendawo mchipatalamo ndipo achemwali a mamunayo ndiwo amadwazika matendawo.
Chomwe chinakwiyitsa kwambiri mamunayo kuti athetse banjalo nchakuti maiyo anamulankhula kuti ‘Inutu m’mene munaliri muja tinakangoika basi.’
Pamene amalanhula izi nkuti m’maso muli gwaa komanso alamu achewo ali onse limodzi.
Koma mkuluyo akuti atapeza bwino ndi kubwelera kunyumba komanso kufunsa anthu nzeru pamau omwe mkazi wakeyo anakamba ali mchipatala anthuwo anamuuza kuti asiye mkaziyo kamba koti sakumufunira zabwino pa moyo wake wa tsiku ndi tsiku.
Apa mamunayo anathamangitsa mkaziyo nkumuuza kuti asadzapondenso pakhomo pake ndipo mkaziyo nayenso anamanga katundu wake ulendo kwa makolo ake.
Padakali pano maiyo akuti wapeza chibwenzi ku Balaka komwe tsopano akukhala komanso kuchita geni ya Makala.