Akwaya Agenda Nyumba Ya M’busa Wawo Patagwa Zovuta

Achinyamata a gulu lina loyimba nyimbo za ambuye akuti masiku apitawa anadabwitsa anthu pamene anakuwiza komanso kugenda nyumba ya m’busa wa pa mpingopo ati kamba koti sanafike pa maliro a m’modzi mwa oyimbao yemwe anatisiya atadwala kanthawi kochepa.
Malinga ndi kunena kwa mkhristu m’modzi pa mpingowo, woyimbayo atamwalira akulu a mpingo ku dera limenelo sanachedwe koma kuthamangila kwa Abusa kukawafotokozera za zovutazo.
Koma akuti pasanapite maola angapo, akulu ampingo ena anapitanso kwa m’busayo ndi kukamuuza kuti malirowo samayenera kuyimbilidwa nyimbo ngakhale kuti omwalirayo anali oyimba kwaya mu limodzi mwa maguluyo.
“Tsiku loyika zovutazo litakwana anthu anayan’ganira kunjira koma m’busayo sanafike ndipo zinamveka kuti wapita kukakhala nawo pa mwambo wa maliro ena kumeneko,” iwo anafotokozera Maravi Express motere ndipo anapitilira nkunena kuti izi sizinasangalatse akhristu a mpingowo makamaka oyimba kwaya omwe amalira nzawoyo.
Zitatha zonse akuti achinyamatawo anatengana ndi kupita pa malo okwelera basi a Chinseu pomwe anadikilira m’busayo kuchokera ku maliro ena omwe anakayimbirawo ndipo atangotsika minibasi pamodzi ndi amayi ena omwe anamuperekeza nayamba kumuyimba nyimbo mpakana kukafika kunyumba.
Madzulo akuti achinyamata omwe akuwaganizira kuti ndi a gulu loyimbalo anayamba kugenda pa denga la nyumba ya m’busayo ndipo sanamupatse tulo olo pang’ono.
Tsiku la sabata litafika m’busayo akuti analengeza mtchalichilo chifukwa chomwe sanapitire ku maliroko kamba koti akulu a mpingo ku dera limenelo anamupomboneza. Pachifukwa ichi m’busayo akuti analamula kuti wachotsa akulu ampingo onse ku dera limenelo ndipo anapempha akhristu kumeneko kuti asankhe ena atsopano.
Kupitiliza apa gulu loyimbalo akutinso walipumisa kwa zaka ziwiri kuti lisayimbenso nyimbo pa mpingowo chinthu chomwe chikuchititsa mantha akhristu kumeneko kuti mwina uku kungakhale kutha kwa gulu loyimbalo.