Awumbuzana Molapitsa Kamba kolimbirana mamuna

Asungwana ena woyendayenda kwa Manje mumzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre kumapeto a sabata yatha akuti anakwapulana molapitsa kamba kolimbirana njonda ina yomwe imachita bizinezi yogulitsa nsomba mumsika wa Limbe.
Malinga ndi kunena kwa mkulu wina yemwe anawona izi zikuchitika maso ndi maso, njondayo yakhala ili pa ubwenzi wamseli ndi m’modzi mwa amayiwo kwa zaka zingapo ndipo akafika pa mabala a kumeneko saumila kunkhani yogula zakumwa zaukali.
Koma masiku apitawa akuti njondayo inapalananso ubwenzi ndi msungwana wina yemwe anangobwera kumene kudzayamba ntchito yodula mowa pa imodzi mwa mabalawo kuchokera m’boma la Mangochi..
“Chomwe chinachitika nchakuti chibwenzi chakale cha mkuluyo chinabisala pa njira kenaka kuyamba kulondolo awiriwo pamene anauyamba ulendo wopita kunyumba kwa mkaziyo. Atangolowa mnyumba nayenso msungwana yemwe amalondola uja anakankha chitseko ndi kulowa ndipo mosakhalitsa chindeu cha dzaoneni chinabuka.
“Khwimbi la anthu linakhamukila panyumbapo kuwonelera chindeucho ndipo anakudzulana madiredi komanso kuvulana zovala mpakana kufika chinochino.
“Apa nkuti mkulu wachimasomasoyo ataliyatsa liwiro la ntondo wodooka kuthawira komwe amakhala,” anafotokoza motere bambo Manyong’onya.
Iwo anapitilira nkunena kuti anyamata ena ndi omwe analetsetsa chindeucho.
Padakali pano, mwini nyumbayo akuti wauza msungwanayo kuti mwezi uno ukatha apakire katundu wake kukafuna nyumba kwina kamba koti safuna maphokoso pa puloti pake.