Apezeleledwa Akuchita za Dama ndi Chibwenzi Atangokwatisa Kumene

Mkulu wina ku Bangwe mumzinda wotchuka kunkhani ya zamalonda wa Blantyre akuti wathawa pa puloti yomwe amakhala kamba koti anamupezelera akuchita za dama ndi msungwana wina yemwe amadula mowa pa bala ina kumeneko.
Izitu akuti zinachitika patangotha masiku awiri mkuluyo atapangitsa ukwati woyera ndi mkazi wake pa mpingo wina kumeneko.
Malinga ndi bambo Faiti omwe atsina khutu Maravi Express za nkhaniyi, mkuluyo yemwe amachita bizinezi ya Nsomba pa msika wa Namatapa akuti anakonza zonse zoyenelera kuti ukwati wake ndi njole yomwe anapezayo ukhale wapamwamba.
“Atadalitsa ukwatiwo, achibale komanso ena akufuna kwabwino anafupa kwambiri komanso kunali kumwa zokumwa zozizilitsa kukhosi ndi zokhwasulakhwasula,” anafotokoza motere bambo Faiti.
Koma akuti patangopita tsiku limodzi, abale ake a mkazi uja anadabwa kuona mkulu uja akulowa mnyumba ya mayi wina woyendayenda ndipo iwo sanachedwe koma kutchayira thenifolo mkazi wa mkuluyo yemwe anafika ndi anzake pa nyumbayo.
Atagogoda akuti mayi woyendayendayo anatsegula koma atangotero mkazi wa mkuluyo ndi achibale aja analowa mnyumbamo momwe anapeza mkulu uja ali gonee pa kama zovala zake zonse zili poteropo.
Atazindikila kuti zinthu zathina mkuluyo akuti anangotola buluku lake nkutulukira pa windo nkuliyatsa liwiro la ntondo wodooka.
Koma mavuto anali m’buyo mwake kamba koti mkazi wa mkulu uja pamodzi ndi abale ake aja anafafantha kwambiri mayi woyendayenda uja nkumuvula zovala zake zonse ndipo anamusiya ali thaphya.
Amayi ena achifundo akuti ndiwo anamuveka chitenje nkumuthawitsa pa nyumbayo.
Padakali pano, mkaziyo akuti wanenetsa kuti banja latsopanolo laumapo ndipo mkwati wachimasomasoyo akuti sakudziwika komwe wathawira.