Ampingo Akana Chakudya Pa Maliro Kamba Koti Sanawapatse Ndiwo Zankhuli

Zina ukamva kamba anga mwala anthuni. Anthu pamudzi wina Mb’oma la Zomba masiku apitawa akuti anadabwa kwambiri pamene akulu ampingo anakhazikika mu nyumba yomwe anawapatsira chakudya kwa nthawi yaitali pa mwambo wina wa zovuta omwe umachitika kamba ka kumwalira kwa gogo wina kumeneko.
Malinga ndi mkulu wina yemwe anafotokozera Maravi Express za nkhaniyi, gogoyo atamwalira anthu anasonkhana pa siwapo kuyembekera ampingo omwenso anafika mwa nthawi yake.
Anthu pa zovutazo akuti analandira chakudya ndipo nawonso akulu a mpingowo anawakonzera chakudya chomwe chinayikidwa mu nyumba ina yoyandikira pa siwapo.
“Koma chomwe chinadabwitsa anthu ndi chakuti ampingowo chiloweleni myumbamo anangoti zii osatulukira pa malirowo kuti zones ziyambike.
“Kenaka anthu anayamba kung’ung’uza ndipo nyakwawa inatuma nduna zake kuti zikaone chomwe chimachitika mnyumbamo ndipo atafika kumeneko anawona kuti akulu ampingo aja angoti jenkha chakudya chija chiri chivindikilireni,” anafotokoza motere mkuluyo.
Ndipo kenaka zinamveka pa malirowo kuti akulu ampingowo amanyinyirika kudya chakudyacho kamba koti ndiwo zake sizinali za nkhuli ngati m’mene iwo amayembekezelera.
Kenaka monyinyilika ena anangotema mbamu zingapo pamene ena anangotuluka nkukakhala pa mwambo wa malirowo.
Mwambo utayambika ndipo itafika nthawi ya zolankhula nyakwawa kumeneko akuti sinabise mawu ponena kuti yakwana nthawi yoti anthu azitha kuzindikira kuti kunja kuno kwagwa chilala ndiponso anthu asamapite ku zovuta ndi cholinga chokafuna kukhutitsa mimba zawo.