Awasamutsa pa Lendi Kamba Koti Mwana Wapha Kazizi

Banja lina ku Mpingwe mtauni ya Blantyre akuti lagwira njakata kamba koti alipatsa masiku kuti lisamuke mu nyumba yomwe likukhala kamba koti mwana wawo anapha Kazizi mumtengo womwe uli pafupi ndi nyumbayo, Maravi Express yamvetsedwa motere.
Malinga ndi kunena kwa mayi Mwandida Phiri omwe amakhala pafupi ndi banjalo, Kaziziyo akuti wakhala akubangula kwa miyezi ingapo yapitayo ndipo wakhala akumauluka kunka m’madenga a nyumba za anthu ena kumeneko.
Koma akuti patsikulo, mwana wa mamuna wa banja lomwe lauzidwa zoti lisamukelo, anatchera msampha pa chisa chomwe Kaziziyo amapezeka mumtengowo ndipo zake zinayenda pamene chimbalamecho chinayamba kubangula ndipo kenaka kunamveka kuphupha kenaka kunangoti zii.
M’mawa kutacha akuti mwanayo analongosolera makolo ake ndi ena oyandikana nawo nyumba kuti wapha Kaziziyo.
Akuti eni nyumba atamva nkhaniyi anakwiya kwambiri ndipo madzulo, makolo a banja lomwe mwana wawo anapha kaziziyo linapatsidwa chikalata kuti asamuke mnyumbayo kamba koti akufuna ayikonze ngakhale kuti ndi yabwino kwambiri polingalira ndi nyumba zina za m’mapuloti.
Anthu kumeneko akuganizira kuti Kaziziyo anali wolenga ndipo amatumidwa m’matsenga popanga zinthu zina ngati kukawa ndalama akamauluka pa denga la nyumba zina.
Banjalo akuti lanenetsa layamba kale kufufuza nyumba kuti lisamuke mwezi kumapeto a mwezi uno.