Adziyipitsira Pambuyo Pomwa Mowa Wachilendo

Mkulu wina ku Bangwe akuti akuyenda werawera pambuyo podziwonongera kamba koti anamwa kwambiri mowa wina wachilendo, Maravi Express yamvetsedwa motere.
Izi akuti zinachitika kumapeto a sabata yatha pa malo ena omwera mowa omwe amatchuka kuti Desert ku Bangwe mumzinda wa Blantyre.
Malinga ndi kunena kwa mkulu wina yemwe amakhala ku Masala wotchedwa Bladson Phimba , mkuluyo akuti wakhala akupapira mowa kwambiri ndipo patsikulo akuti atangoweluka ku ganyu yake anaganiza zokamwa mowa wachilendowo ndi anzake.
“Pambuyo pokhuta kwambiri iye anauyamba ulendo wopita kunyumba koma panjira anagwa mpakana kudziwonongela komanso kukozedwa.
“M’mene zimachitika izi nkuti ana nawonso akumuyimba nyimbo ndipo kenaka azinzake anamutengela kunyumba kwake komwe anamusambisa,” a Phimba anauza Maravi Express motere.
Mkuluyo akuti wanenetsa kuti sazamwanso mowa wachilendowo koma mbili kumeneko akuti ili buuu! ndipo akuyenda werawera ngati nkuku ya Chitopa kamba ka manyazi.