Asesa Katundu Yense Atapezelera Mamuna Wake Akuchita Za Dama ndi Chibwenzi Likuswa Mtengo

Mayi wina ku Nguludi m’boma la la Chiradzulu akuti masiku apitawa anasesa ndi kunyamula katundu yense wa mnyumba ulendo kumudzi kwawo atapezelera mamuna wake akuchita za dama ndi mayi wina woyendayenda dzuwa likuswa mtengo m’matolo.
Malinga ndi kunena kwa bambo Alick Phinifolo omwe amachita geni yowoda nkhuku nkumagulitsa ku Limbe, nkhaniyi yati maiyo wakhala akukayikila mayendedwe a mamuna wakeyo atatsinidwa khutu kuti anthu akhala akuwona ndi kamtsikana kena koyendayenda koma mkuluyu akuti wakhala akukanitsitsa kwantu wa galu akamufunsa.
Ndiye paja akulu amati ukatambatamba udziyamba wapenya kunyanja kamba koti kungakuchere, mkuluyo patsikulo zake zinamudera pamene anatsanzika mkazi wakeyo kuti wayamba wapita ku dimba kukawona mbeu.
Koma akuti awiriwo anali atagwirizana kuti akakumane ku matoloko kuti akapange zadamazo.
Mkuluyo ali ku matoloko, pakhomopo panafika mlendo yemwe anafuna kukambirana naye ndipo mayi wa pakhomopo anapatsa mlendoyo thobwa nkuuyala ulendo wokaitana bamboyo ku matoloko.
Koma akuti atafika ku matoloko, mkuluyo sanawoneke ndipo maiyo anamva mau pa tchire lina loyandikila matolowo ndipo anaganiza zokawona kuti mwina angakgale anthu akuba nzimbe.
Atangolowa pa tchirepo akuti anapeza mkuluyo akuchita za dama ndi msungwana woyendayendayo ndipo bamboyo akuti analiyala liwiro kulowera mu nkhalango ina atangotsala ndi kabudula wa mkati yekha.
Apa maiyo anayamba kufafantha msungwanayo molapitsa kwinaku akukuwa ndipo mosakhalitsa anthu ena omwenso anali m’matolo mwawo anathamangira komweko komwe nawonso analanga msungwanayo nkumung’ambira zovala zake zonse nkumusiya ali chinochino.
Mai wina wachifundo ndi yemwe anapereka chitenje kwa msungwanayo yemwe amatuluka magazi mphuno ndi mkamwa komanso nkhope yonse inali itatupiratu.
Zitangochitika izi, maiyo akuti anakauza akwawo omwe anabwera pa njinga nkusesa katundu yense wa mnyumbamo.
Padakali pano, mkulu wachimasomasoyo akuti sakudziwika komwe ali kamba ka manyazi ndi nkhaniyi.