Amangililidwa M’mitengo ku Manda Kamba ka Chibwana cha Nchombo Lende

Amuna atatu posachedwapa akuti anamangililidwa m’mitengo ku manda m’boma la Phalombe kamba koledzera mosachita bwino pamene mwambo wa maliro unali mkati kumeneko.
Malinga ndi bambo Mark Phinifolo omwe anafotokozera Maravi Express za nkhaniyi, anthu anali odabwa pamene anyamata ena omwe ndi achibale a malemuyo omwe amakhala mumzinda wa Blantyre akuti anakhuta kwambiri bibida pamene anthu komanso a mpingo amakhazika zovutazo pa siwapo.
Ndipo kutacha makosanawo akuti sanalekere pomwepo koma anapitilizabe kuudadanya mowa kenaka anapita kukakhala nawo pa mwambo wa malirowo.
Itafika nthawi yoti zovutazo zikayikidwe ku manda, anyamatawo akuti anapita ku mandako komwe anayamba kusokoneza ndipo mosakhalitsa adzukulu ena anagwira ndikuwamangilira anyamatawo m’mitengo.
M’mene izi zimachitika ndi kuti mwambo wa zovutazo uli mkati.
Zithatha zonse akuti amfumu polankhula anauza makolo a zidakwazo pamodzi ndi anyamatawo kuti akakumane nawo pa bwalo tsiku lotsatira.
Pamene Maravi Express imatsindikiza za nkhaniyi nkuti zisakudziwika kuti zawathera bwanji kumeneko.