Zigandanga ziphedwa kamba kofuna KUbera Anthu

Malipoti omwe afikila Maravi Express akuti anamalira pa Tauni agagada ndi kupha anthu atatu omwe amawaganizira kuti ndi mbava.
Izitu zachitika mu limodzi la maboma a mdziko lino mchigawo chakumwera.
Malinga ndi kunena kwa mayi Eneya, mbavazo zinagagadidwa atazigwira pamene zimafuna kuba pa ina mwa sitolo za pamalopo.
Apolisi atsimikiza za nkhaniyi ndipo auza anthu kuti azipita mwamsanga kukanena ku polisiko ngati ataganizira munthu kuti ndi tsinzinantole.
Miyezi yapitayi apolisi akhwimitsa chitetezo m’maboma ambiri mdziko muno.
Nawonso anthu sakulola kamba koti monga m’mene anayimbira nyimbo uja otchuka Phungu Joseph Nkasa kuti mukaguwira mbava ikong’ontheni ndipo izi zikuchitikadi.